Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 45

Ufumu Unagawikana

Ufumu Unagawikana

Pamene Solomo ankalambira Yehova, ku Isiraeli kunali mtendere. Koma kenako anakwatira akazi ambiri a mitundu ina ndipo akaziwa ankalambira mafano. Pang’ono ndi pang’ono, Solomo anasintha ndipo nayenso anayamba kulambira mafano. Yehova anakwiya kwambiri ndi zimenezi. Ndiyeno anauza Solomo kuti: ‘Ufumu wa Isiraeli uchotsedwa ku banja lako ndipo ugawikana pawiri. Ndidzapereka mbali yaikulu ya ufumuwu kwa mtumiki wako ndipo banja lako lidzatsala ndi mbali yochepa.’

Yehova anachitanso zinthu zina posonyeza kuti zimenezi zidzachitikadi. Tsiku lina, mtumiki wina wa Solomo, dzina lake Yerobowamu anali pa ulendo ndipo anakumana ndi mneneri Ahiya. Ahiya anang’amba chovala chake zidutswa zokwana 12. Atatero anauza Yerobowamu kuti: ‘Yehova achotsa ufumu wa Isiraeli ku banja la Solomo ndipo augawa pawiri. Tenga zidutswa 10 izi chifukwa iweyo udzakhala mfumu ya mafuko 10.’ Mfumu Solomo atamva zimenezi, anafuna kupha Yerobowamu. Choncho Yerobowamu anathawira ku Iguputo. Patapita nthawi, Solomo anamwalira ndipo mwana wake Rehobowamu anakhala mfumu. Zitatero Yerobowamu anaona kuti akhoza kubwerera ku Isiraeli.

Akuluakulu a ku Isiraeli anauza Rehobowamu kuti: ‘Mukamawalamulira bwino anthuwa, akhala okhulupirika kwa inu.’ Koma achinyamata anzake anamuuza kuti: ‘Anthuwa musamawalamulire mowanyengerera. Muziwagwiritsa ntchito zolemetsa kuposa zimene bambo anu ankawagwiritsa.’ Rehobowamu anamvera malangizo amenewa. Choncho ankalamulira anthuwo mwankhanza ndipo iwo anamuukira. Anthuwo anasankha Yerobowamu kuti akhale mfumu ya mafuko 10, omwe ankadziwika kuti ufumu wa Isiraeli. Mafuko awiri okha ndi amene anakhalabe okhulupirika kwa Rehobowamu ndipo ankadziwika kuti ufumu wa Yuda. Apa ndiye kuti mafuko 12 a Aisiraeli anagawikana.

Yerobowamu sankafuna kuti anthu ake azipita kukalambira ku Yerusalemu kumene mfumu yake anali Rehobowamu. Ukudziwa chifukwa chake? Yerobowamu ankaopa kuti anthuwo akhoza kumuukira n’kupita kumbali ya Rehobowamu. Choncho anapanga mafano awiri a ana a ng’ombe n’kuuza anthuwo kuti: ‘Muzilambirira konkuno, chifukwatu ku Yerusalemu n’kutali.’ Ndiyeno anthuwo anayambadi kulambira ana a ng’ombewo ndipo anaiwala Yehova.

“Musamangidwe m’goli ndi osakhulupirira, chifukwa ndinu osiyana. Pali ubale wotani pakati pa chilungamo ndi kusamvera malamulo? . . . Kapena munthu wokhulupirira angagawane chiyani ndi wosakhulupirira?”​—2 Akorinto 6:14, 15