Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 45

Ufumu Ugaŵika

Ufumu Ugaŵika

Pamene Solomo anali kulambila Yehova mokhulupilika, mu Isiraeli munali mtendele. Koma m’kupita kwa nthawi, Solomo anakwatila akazi ambili ocokela ku mitundu ina yolambila mafano. Pang’ono m’pang’ono Solomo anasintha, mpaka nayenso anayamba kulambila mafano. Yehova anakwiya kwambili, cakuti anauza Solomo kuti: ‘Ufumu wa Isiraeli udzacotsedwa ku banja lako, ndipo nidzaugaŵa paŵili. Gawo lalikulu nidzapatsa mmodzi wa atumiki ako, banja lako lidzangolamulila gawo locepa.’

Yehova anaonetsanso cigamulo cakeci mwa njila ina. Tsiku lina Yeroboamu, mmodzi wa atumiki a Solomo ali pa ulendo, anakumana na mneneli Ahiya. Ahiya anang’amba covala cake m’zidutswa 12, ndipo anauza Yeroboamu kuti: ‘Yehova adzacotsa ufumu wa Isiraeli ku banja la Solomo na kuugaŵa paŵili. Tenga zidutswa 10 izi, cifukwa udzakhala mfumu ya mafuko 10.’ Mfumu Solomo atamvela zimenezi, anafuna kumupha Yeroboamu! Anacita kuthaŵila ku Iguputo. M’kupita kwa nthawi, Solomo anamwalila, ndipo mwana wake Rehoboamu anakhala mfumu. Apa lomba, Yeroboamu anaona kuti akhoza kubwelela ku Isiraeli.

Akulu-akulu acisiraeli anauza Rehoboamu kuti: ‘Ngati mudzaŵalamulila bwino anthu awa, adzakhala okhulupilika kwa inu.’ Koma anzake acinyamata a Rehoboamu anati: ‘Anthu amenewa osawalamulila moŵanyengelela! Muziŵagwilitsa nchito zolemetsa kuposa zimene atate anu anali kuwapatsa.’ Rehoboamu anatsatila malangizo a anyamata anzake. Anali wankhanza kwa anthu, ndipo anthuwo anamuukila. Anthuwo anasankha Yeroboamu kukhala mfumu ya mafuko 10, ndipo unachedwa ufumu wa Isiraeli. Mafuko ena aŵili anachedwa kuti ufumu wa Yuda, ndipo anthu ake anakhala okhulupilika kwa Rehoboamu. Uku ndiye kunali kugaŵika kwa mafuko 12 a Isiraeli.

Yeroboamu sanafune kuti anthu ake azikalambila ku Yerusalemu, kwa mfumu Rehoboamu. Udziŵa cifukwa cake? Anali kuyopa kuti anthu ake angam’pandukile na kukhala kumbali ya Rehoboamu. Conco, anapanga ana a ng’ombe agolide aŵili na kuuza anthu ake kuti: ‘Ku Yerusalemu ni kutali kwambili. Muzilambilila kuno.’ Anthuwo anayambadi kulambila ana a ng’ombe agolide, na kumuiŵalanso Yehova.

“Musamangidwe m’goli ndi osakhulupilila, cifukwa ndinu osiyana. Pali ubale wotani pakati pa cilungamo ndi kusamvela malamulo? . . . Kapena munthu wokhulupilila angagawane ciyani ndi wosakhulupilila?”—2 Akorinto 6:14, 15