Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 46

Zimene Zinachitika Paphiri la Karimeli

Zimene Zinachitika Paphiri la Karimeli

Ufumu wa mafuko 10 wa Isiraeli unali ndi mafumu ambiri oipa. Koma Mfumu Ahabu ndi amene anali woipa kuposa onsewo. Iye anakwatira mkazi woipa amene ankalambira Baala ndipo dzina lake anali Yezebeli. Ahabu ndi Yezebeli ankapha aneneri a Yehova komanso anapangitsa kuti anthu ambiri a ku Isiraeli azilambira Baala. Ndiye kodi Yehova anatani? Anatumiza mneneri Eliya kuti akapereke uthenga kwa Ahabu.

Eliya anauza mfumuyi kuti popeza inkachita zoipa, m’dziko la Isiraeli simugwa mvula. Kwa zaka zoposa zitatu anthu sanathe kulima chakudya chifukwa kunali chilala. Choncho m’dzikolo munagwa njala. Kenako Yehova anatumizanso Eliya kwa Ahabu. Ndiyeno mfumuyo inati: ‘Iwe ndi amene wabweretsa mavuto onsewa.’ Koma Eliya anayankha kuti: ‘Ayi si ine. Mwabweretsa chilalachi ndi inuyo chifukwa mukulambira Baala. Sonkhanitsani anthu ndi aneneri a Baala pamwamba pa phiri la Karimeli kuti tikaone umboni wa zimenezi.’

Anthu anasonkhanadi paphirilo. Ndiyeno Eliya anawauza kuti: ‘Sankhani Mulungu woti muzimulambira. Ngati Yehova ndiye Mulungu woona, m’tsateni, koma ngati Baala ndiye Mulungu woona tsatirani ameneyo. Atumiki 450 a Baala akonze nsembe ndipo apemphere kwa mulungu wawo kuti apsereze nsembeyo. Inenso ndikonza nsembe yanga ndipo ndipemphera kwa Yehova kuti aipsereze. Mulungu amene angathe kupserezadi nsembezi ndiye woona.’ Anthuwo anavomera.

Aneneri a Baala anakonzadi nsembe yawo. Anapemphera kwa mulungu wawo tsiku lonse kuti: ‘Inu a Baala tiyankheni!’ Koma Baala sanawayankhe. Kenako Eliya anayamba kuwaseka. Anawauza kuti: ‘Muitaneni mokweza. Mwina wagona ndipo pakufunika wina amudzutse.’ Aneneri a Baala anapitirizabe kupemphera mpaka madzulo koma Baalayo sanawayankhe.

Kenako Eliya anaika nsembe yake paguwa ndipo anathirapo madzi. Ndiyeno anapemphera kuti: ‘Yehova, ndikukupemphani kuti muchite zoti anthuwa adziwe kuti ndinu Mulungu woona.’ Nthawi yomweyo Yehova anatumiza moto kuchokera kumwamba ndipo unapsereza nsembeyo. Anthu ataona zimenezi anayamba kufuula kuti: ‘Yehova ndiye Mulungu woona.’ Eliya anati: ‘Gwirani aneneri onse a Baala.’ Pa tsikuli aneneri onse a Baala okwana 450 anawagwira n’kuwapha.

Kenako kunyanja kunaoneka kamtambo kakang’ono ndipo Eliya anauza Ahabu kuti: ‘Kugwa chimvula champhamvu. Kwerani galeta muzipita kwanu.’ Mwadzidzidzi kunja kunachita mdima wa mitambo, kunayamba kuwomba chimphepo ndipo kenako chimvula chinayamba kugwa. Apa ndiye kuti chilala chija chinatha. Ahabu anayamba kuthamangitsa galeta lake n’cholinga choti chimvulacho chisamutsekereze. Koma mothandizidwa ndi Yehova, Eliya anathamanga mpaka kupitirira galeta la Ahabu lija. Ndiye kodi mavuto a Eliya anathera pamenepa? Tiona m’nkhani yotsatira.

“Anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.”​—Salimo 83:18