Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 47

Yehova Analimbikitsa Eliya

Yehova Analimbikitsa Eliya

Yezebeli atamva zimene zinachitikira aneneri a Baala, anakwiya kwambiri. Ndiyeno anatumiza uthenga kwa Eliya wakuti: ‘Mawa nawenso ufa ngati mmene afera aneneri a Baala.’ Eliya atamva zimenezi anachita mantha kwambiri ndipo anathawira kuchipululu. Kumeneko anapemphera kuti: ‘Yehova, zimene zikuchitikazi ndatopa nazo. Ndiloleni kuti ndingofa.’ Chifukwa chotopa Eliya anagona tulo pansi pa mtengo.

Ndiyeno kunabwera mngelo n’kumugwedeza ndipo anamuuza kuti: ‘Dzuka udye.’ Eliya atayang’ana, anaona chikho cha madzi komanso mkate wozungulira uli pamiyala yotentha. Anadya mkatewo n’kumwa madziwo ndipo kenako anagonanso. Patapita nthawi, mngelo uja anabweranso kudzamudzutsa n’kumuuza kuti: ‘Idyanso kuti upeze mphamvu chifukwa uyenda ulendo wautali.’ Choncho Eliya anadzuka n’kudyanso. Kenako anayenda kwa masiku 40, usana ndi usiku mpaka kukafika paphiri la Horebe. Ndiyeno analowa kuphanga n’kugona. Koma Yehova anamufunsa kuti: ‘Ukufuna chiyani kuno Eliya?’ Eliya anayankha kuti: ‘Aisiraeli aswa pangano lawo ndi inu. Agwetsa maguwa anu ansembe, ndipo apha aneneri anu. Panopa akufunanso kundipha ineyo.’

Koma Yehova anamuuza kuti: ‘Pita ukaime paphiri.’ Ndiyeno panawomba chimphepo kudutsa pakhomo la phangalo. Kenako kunachita chivomezi ndipo pambuyo pa chivomezicho, kunabuka moto. Zitatere Eliya anamva mawu achifatse apansipansi. Atangomva mawuwo, anaphimba nkhope yake ndi chovala chake ndipo anatuluka n’kukaima pakhomo la phanga lija. Yehova anamufunsanso kuti: ‘Ukufuna chiyani kuno?’ Eliya anayankha kuti: ‘Ndatsala ndekhandekha.’ Koma Yehova anamuuza kuti: ‘Suuli wekha. Mu Isiraeli mulinso anthu ena okwana 7,000 amene akundilambirabe. Pita ukadzoze Elisa kuti adzalowe m’malo mwako.’ Nthawi yomweyo Eliya anapita kukachita zimene Yehova anamuuzazo. Kodi ukuganiza kuti nawenso Yehova angakuthandize ukamachita zimene amafuna? Inde angakuthandize. Tsopano tiye tione zimene zinachitika pa nthawi yachilala.

“Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.”​—Afilipi 4:6