Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 48

Mwana wa Mkazi Wamasiye Aukitsidwa

Mwana wa Mkazi Wamasiye Aukitsidwa

Pa nthawi ya cilala, Yehova anauza Eliya kuti: ‘Pita ku Zarefati. Kumeneko mkazi wamasiye adzakupatsa cakudya.’ Atangolowa mu mzinda, Eliya anaona mkazi wamasiye akutola nkhuni. Iye anapempha mzimayiyo madzi akumwa. Pamene mzimayiyo ananyamuka kuti akatenge madzi, Eliya anam’pemphanso kuti: ‘Conde, unibweletselekonso mkate.’ Koma mzimayiyo anati: ‘Nilibe mkate wakuti nikupatseni. Nili na tufulawo tocepa cabe, komanso tumafuta tongokwanila ine na mwana wanga.’ Eliya anamuuza kuti: ‘Yehova walonjeza kuti ngati unipangila mkate, fulawo wako na mafutawo sadzatha mpaka mvula ikabwele.’

Conco, mkazi wamasiyeyo anapita ku nyumba kukakonzela mkate mneneli wa Yehova. Monga mmene Yehova analonjezela, mzimayiyo na mwana wake, cakudya sicinawathele m’nthawi yonse ya cilala. Mtsuko wake wa fulawo komanso wa mafuta sunapunguke.

Koma panacitika cinthu cina coipa kwambili. Mwana wa mzimayiyo anadwala kwambili mpaka anamwalila. Mkaziyo anapempha Eliya kuti am’thandize. Eliya anatenga mwanayo m’manja mwa mayi ake n’kupita naye kucipinda cinali pamwamba. Anam’goneka pa bedi, na kupemphela kuti: ‘Yehova, conde muukitseni mwanayu.’ Zimene Eliya anapempha zinali zocititsa cidwi kwambili. Udziŵa cifukwa cake? Cifukwa mmene tidziŵila, kumbuyo konseko kunalibe munthu amene anaukitsidwapo. Komanso, mkazi wamasiyeyu na mwana wake sanali Aisiraeli n’komwe.

Mwanayo anauka, ndipo anayambanso kupuma! Eliya anauza mkaziyo kuti: ‘Ona! Mwana wako wakhalanso na moyo.’ Mkaziyo anasangalala kwambili, ndipo anauza Eliya kuti: ‘Ndinu munthu wa Mulungu zoona. Nadziŵa, cifukwa mumakamba mawu amene Yehova wakuuzani, ndipo mawuwo amakwanilitsikadi.’

“Onetsetsani makwangwala, iwo safesa mbewu kapena kukolola. Alibe nyumba yosungilamo zinthu kapena nkhokwe, komatu Mulungu amawadyetsa. Kodi inu si ofunika kwambili kuposa mbalame?”—Luka 12:24