Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 49

Mfumukazi Yoipa Inalangiwa

Mfumukazi Yoipa Inalangiwa

Mfumu Ahabu akakhala pa windo ya nyumba yake yacifumu ku Yezereeli, anali kuona munda wampesa wa munthu wina dzina lake Naboti. Ahabu anafuna kuti mundawo ukhale wake. Anapempha Naboti kuti am’gulitse mundawo. Koma Naboti anakana, cifukwa kugulitsa colowa kunali kosaloleka m’Cilamulo ca Yehova. Kodi Ahabu anaona kuti Naboti wacita cinthu coyenela? Kutalitali! Ahabu anakalipa maningi cakuti sanali kucoka m’cipinda cake cogona, ngakhale kudya anali kukana.

Koma mkazi wa Ahabu, Mfumukazi yoipa Yezebeli, inauuza mwamuna wake kuti: ‘Ndimwe mfumu ya Isiraeli. Ciliconse cimene mufuna cingakhale canu. Ine nidzakutengelani mundawo kuti ukhale wanu.’ Mwa ici, analemba makalata kwa akulu a mzindawo, n’kuwauza kuti anamizile Naboti kuti wanyoza Mulungu, conco afunikila kuphedwa mwa kum’ponya miyala. Akuluwo anacita zimene Yezebeli anawauza. Kenako Yezebeli anauza Ahabu kuti: ‘Naboti wafa. Munda wampesa uja ni wanu manje.’

Si Naboti yekha amene Yezebeli anamupha popanda cifukwa. Anapha anthu ambili okonda Yehova. Iye anali kulambila mafano na kucitanso zinthu zambili zoipa. Yehova anali kuona zinthu zonse zoipa zimene Yezebeli anali kucita. Kodi Yehova anacitapo ciani?

Ahabu atamwalila, m’kupita kwa nthawi mwana wake Yehoramu anakhala mfumu. Yehova anatumiza munthu wina dzina lake Yehu, kuti akalange Yezebeli na banja lake.

Yehu anathamangitsa galeta lake kupita ku Yezereeli kumene Yezebeli anali kukhala. Yehoramu anapita na galeta lake kukakumana na Yehu, ndipo anam’funsa kuti: ‘Kodi mwabwelela mtendele?’ Yehu anayankha kuti: ‘Sipangakhale mtendele pamene mayi wako Yezebeli akucita zinthu zoipa.’ Yehoramu anayesa kutembenuza galeta lake kuti athaŵe. Koma Yehu anamulasa na muvi, ndipo anafela pamenepo.

Kenako Yehu anayenda ku nyumba yacifumu ya Yezebeli. Yezebeli atamvela kuti Yehu akubwela, anayamba kudzikongoletsa, kukonza tsitsi lake, na kukayembekezela pa windo ya cipinda capamwamba. Yehu atafika, Yezebeli anayamba kukamba naye mwamwano. Pamenepo Yehu anafuula kwa anchito a Yezebeli amene anali naye pafupi. Iye anati: “M’ponyeni pansi!” Iwo anamunyamula na kum’ponya pa windopo, cakuti anagwa pansi n’kufela pamenepo.

Pambuyo pa izi, Yehu anapha ana a Ahabu okwana 70, na kufafanizilatu kulambila kwa Baala. Kodi waona kuti Yehova amadziŵa zonse, ndipo amacita zinthu pa nthawi yake, komanso amalanga amene amacita zoipa?

“Colowa copezedwa mwadyela poyamba, tsogolo lake silidzadalitsidwa.”—Miyambo 20:21