Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 50

Yehova Anateteza Yehosafati

Yehova Anateteza Yehosafati

Yehosafati mfumu ya Yuda, anawononga maguwa ansembe a Baala na mafano ake onse. Anafuna kuti anthu adziŵe malamulo a Yehova. Conco anatuma zinduna komanso Alevi ku madela onse a ufumu wa Yuda, kuti akaphunzitse anthu cilamulo ca Yehova.

Mitundu yapafupi inali kuyopa kuukila Ayuda, cifukwa inali kudziŵa kuti Yehova ali kumbali yawo. Anali kucita kubweletsa mphatso kwa Mfumu Yehosafati. Koma Amoabu, Aamoni na ena ocokela ku cigawo ca Seiri anabwela kudzacita nkhondo na Ayuda. Yehosafati anadziŵa kuti anafunikila thandizo la Yehova. Iye anasonkhanitsa amuna, akazi, ndi ana ku Yerusalemu. Ataimilila pamaso pa onse, anapemphela kuti: ‘Yehova, popanda imwe sitingapambane. Conde tiuzeni zocita.’

Yehova anayankha pemphelo limeneli. Iye anati: ‘Musacite mantha. Nidzakuthandizani. Khalani m’malo anu, imani cilili na kuona mmene nikupulumutsileni.’ Kodi Yehova anawapulumutsa bwanji?

M’mawa mwake, Yehosafati anasankha anthu oimba, na kuwauza kuti aziimba kutsogolo kwa asilikali. Iwo anayenda kucokela ku Yerusalemu mpaka kumalo omenyela nkhondo ochedwa Tekowa.

Pamene oimba anali kutamanda Yehova mosangalala komanso mokweza mawu, Yehova anamenyela nkhondo anthu ake. Anapangitsa Aamoni na Amoabu kusokonezeka, cakuti anayamba kuphana okha-okha, ndipo sipanapulumuke olo mmodzi. Koma Yehova anateteza Ayuda, asilikali, komanso ansembe. Anthu onse m’maiko ozungulila anamvela zimene Yehova anacita. Ndipo anadziŵa kuti Yehova ndiye anali kuteteza anthu ake. Kodi Yehova amapulumutsa bwanji anthu ake? M’njila zambili. Ndipo iye safunikila thandizo la munthu.

“Ulendo uno simufunikila kumenya nkhondo. Khalani m’malo anu, imani cilili ndi kuona Yehova akukupulumutsani.”—2 Mbiri 20:17