Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 52

Gulu Lamphamvu la Asilikali a Yehova

Gulu Lamphamvu la Asilikali a Yehova

Beni-hadadi anali mfumu ya Siriya ndipo ankakonda kupita kukamenyana ndi Aisiraeli. Koma nthawi zonse mneneri Elisa ankadziwitsa mfumu ya Isiraeli ndipo mfumuyo inkathawa. Ndiyeno Beni-hadadi anaganiza zotuma asilikali ake kuti akagwire Elisa. Iye anamva kuti Elisayo ali ku Dotana.

Asilikali a Siriya anafika ku Dotana usiku n’kuzungulira mzindawo. M’mawa, mtumiki wa Elisa atatuluka panja anaona gulu la asilikalilo. Iye anachita mantha kwambiri ndipo anafuula kuti: ‘Mayo ine! Titani pamenepa ambuye?’ Koma Elisa anamuuza kuti: ‘Usaope, ifetu tili ndi ambiri kuposa amene ali ndi iwowo.’ Ndiyeno Yehova anatsegula maso a mtumikiyo ndipo anaona kuti m’mapiri onse ozungulira mzindawo munali mahatchi ndi magaleta ankhondo oyaka moto.

Pamene asilikali a Siriya ankafuna kugwira Elisa, iye anapemphera kuti: ‘Chonde Yehova achititseni khungu.’ Mwadzidzidzi, asilikali aja anapezeka kuti sakuzindikira kumene ali ngakhale kuti ankaona. Zitatero Elisa anawauza kuti: ‘Mwasocheratu. Bwerani kuno ndikuperekezeni kwa munthu amene mukufuna.’ Asilikaliwo anayamba kumutsatira mpaka kukafika ku Samariya kumene mfumu ya Aisiraeli inkakhala.

Apa m’pamene asilikaliwo anazindikira kumene ali. Mfumuyo itawaona inafunsa Elisa kuti: ‘Kodi ndiwaphe?’ Kodi Elisa anaona ngati umenewu unali mwayi woti aphe anthuwa? Ayi. M’malomwake anauza mfumuyo kuti: ‘Musawaphe. Apatseni chakudya adye kenako muwalole kuti azipita.’ Choncho mfumuyo inawakonzera phwando lalikulu. Atatha kudya ananyamuka n’kumapita kwawo.

“Ifetu timamudalira kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.”​—1 Yohane 5:14