Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 53

Yehoyada Anali Wolimba Mtima

Yehoyada Anali Wolimba Mtima

Yezebeli anali ndi mwana wamkazi dzina lake Ataliya. Mwanayu anali woipa ngati mayi ake. Ataliya anakwatiwa ndi mfumu ya Yuda. Mwamuna wake atamwalira, mwana wake wamwamuna anakhala mfumu. Ndiyeno mwana wakeyo atamwaliranso, Ataliya anayamba kulamulira. Iye anayesetsa kupha anthu onse akubanja lachifumu amene akanalowa ufumu. Anapha ngakhale adzukulu ake ndipo anthu onse ankamuopa kwambiri.

Mkulu wa Ansembe Yehoyada ndi mkazi wake Yehoseba anadziwa kuti zimene Ataliya ankachitazi zinali zoipa. Choncho anatenga Yehoasi, yemwe anali mdzukulu wake wa Ataliya, n’kukamubisa m’kachisi. Anachita zimenezi ngakhale kuti ankadziwa zoti Ataliya akazindikira akhoza kuwapha.

Yehoasi atakwanitsa zaka 7, Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a magulu a asilikali ndi Alevi n’kuwauza kuti: ‘Muime pamakomo a kachisi ndipo muonetsetse kuti aliyense asalowe muno.’ Ndiyeno Yehoyada anamuika Yehoasi kukhala mfumu ya Yuda n’kumuveka chipewa chachifumu. Atatero, Ayuda anafuula kuti: ‘Mfumu ikhale ndi moyo wautali!’

Ataliya atamva phokoso la anthu, anathamangira kukachisi. Ataona mfumu yatsopanoyo, anafuula kuti: ‘Mwandichitira chiwembu! Mwandichitira chiwembu!’ Zitatero atsogoleri a asilikali aja anamugwira n’kumutulutsira kunja ndipo anakamupha. Koma Ataliya anali atasocheretsa kwambiri Ayuda.

Ndiye kodi Yehoyada anatani? Iye anathandiza kuti Ayuda achite pangano ndi Yehova ndipo analonjeza kuti azilambira iye yekha. Anawauzanso kuti akagwetse kachisi wa Baala n’kuphwanya mafano onse. Kuwonjezera apo, anasankha ansembe ndi Alevi oti azitumikira pakachisi kuti anthu ayambirenso kulambira Yehova. Ndiponso anaika alonda oti azikhala pageti n’cholinga choti azionetsetsa kuti aliyense wodetsedwa asalowe. Ndiyeno Yehoyada ndi atsogoleri a magulu a asilikali aja anatenga Yehoasi n’kupita naye kunyumba yachifumu ndipo anamukhazika pampando. Ayuda anasangalala kwambiri. Apa tsopano iwo akanatha kulambira Yehova bwinobwino, popanda kuopsezedwa ndi Ataliya kapena kusokonezedwa ndi anthu olambira Baala. Kulimba mtima kwa Yehoyada kunathandiza anthu ambiri.

“Musachite mantha ndi amene amapha thupi koma sangaphe moyo, m’malomwake, muziopa iye amene angathe kuwononga zonse ziwiri, moyo ndi thupi lomwe m’Gehena.”​—Mateyu 10:28