Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 53

Yehoyada Anali Wolimba Mtima

Yehoyada Anali Wolimba Mtima

Yezebeli anali na mwana wamkazi dzina lake Ataliya, amenenso anali woipa monga amayi ake. Ataliya anakwatiwa kwa mfumu ya Yuda. Pamene mwamuna wake anamwalila, mwana wake wamwamuna anayamba kulamulila. Koma pamene mwanayo anamwalila, Ataliya anadziika kukhala mfumu ya Yuda. Ndiyeno anayesetsa kuwononga mzele wonse wa mafumu, mwa kupha aliyense amene angakhale mfumu m’malo mwa iye. Anaphanso ngakhale adzukulu ake aamuna. Aliyense anali kumuopa.

Mkulu wa Ansembe Yehoyada na mkazi wake Yehoseba, anali kudziŵa kuti zimene Ataliya anali kucita zinali zoipa kwambili. Iwo anaika miyoyo yawo paciswe mwa kubisa mwana wakhanda dzina lake Yehoasi, mdzukulu wa Ataliya. Anam’sungila mu kacisi.

Pamene Yehoasi anafika zaka 7, Yehoyada anasonkhanitsa atsogoleli na Alevi onse, n’kuwauza kuti: ‘Musalole aliyense kuloŵa m’kacisi.’ Ndiyeno Yehoyada anadzoza Yehoasi kukhala mfumu ya Yuda, na kumuveka cisoti cacifumu. Pamenepo Ayuda anafuula kuti: ‘Moyo wautali kwa Mfumu!’

Mfumukazi Ataliya atamvela congo cimeneco, anathamangila ku kacisi. Ataona mfumu yatsopano, anafuula kuti: “Ciwembu! Ciwembu!” Pamenepo atsogoleli anagwila mfumukazi yoipayo, anatuluka nayo panja na kuipha. Nanga bwanji za kulambila konyenga kumene Ataliya anayambitsa?

Yehoyada anathandiza Ayuda kuti acite cipangano na Yehova, cakuti azilambila Iye yekha basi. Pomvela Yehoyada, anthuwo anaphwanya kacisi wa Baala na mafano ake onse. Yehoyada anasankha ansembe komanso Alevi kuti azitumikila pa kacisi, kuti anthu ayambenso kulambila pa kacisi. Anaikanso alonda pa mageti a kacisi, kuti asalole munthu aliyense wodetsedwa kuloŵa. Ndiyeno Yehoyada pamodzi na atsogoleli, anatenga Yehoasi kupita naye ku nyumba yacifumu kukamukhazika pa mpando wacifumu. Ayuda anakondwela kwambili. Apa lomba iwo anayambanso kutumikila bwino Yehova, atamasuka kwa Ataliya woipayo, kunalibenso zolambila Baala. Kodi waona kuti kulimba mtima kwa Yehoyada kunathandiza anthu ambili?

“Musacite mantha ndi amene amapha thupi koma sangaphe moyo, m’malomwake, muziopa iye amene angathe kuwononga zonse ziwili, moyo ndi thupi lomwe m’Gehena.”—Mateyu 10:28