Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 57

Yehova Anauza Yeremiya Kuti Azilalikira

Yehova Anauza Yeremiya Kuti Azilalikira

Yehova anauza Yeremiya kuti azilalikira kwa Ayuda. Anamuuza kuti aziwachenjeza kuti asiye kuchita zoipa. Koma Yeremiya anayankha kuti: ‘Yehova, ndine mwanatu. Sindingathe kulalikira kwa anthu amenewa.’ Ndiyeno Yehova anamuuza kuti: ‘Usaope. Ndikuuza zonse zoti uzinena ndipo ndikuthandiza.’

Yehova anauza Yeremiya kuti asonkhanitse akuluakulu onse, kenako aswe botolo ladothi iwo akuona ndipo awauze kuti: ‘Yerusalemu adzaswedwa chonchi!’ Yeremiya atachita zimenezi, akuluakuluwo anakwiya kwambiri. Wansembe wina dzina lake Pasuri anamenya Yeremiya kenako n’kumuika m’matangadza. Yeremiya anakhalamo usiku wonse ndipo sankatha kuyenda. M’mawa kutacha Pasuri anamasula Yeremiya m’matangadzamo ndipo Yeremiya anati: ‘Zimene akundichitazi zandikwana. Basi sindilalikiranso.’ Koma kodi Yeremiya anasiyadi kulalikira? Ayi. Ataiganizira bwinobwino nkhaniyi anati: ‘Uthenga wa Yehova uli ngati moto mumtima mwanga moti sindingathe kusiya kulalikira.’ Choncho Yeremiya anapitiriza kuchenjeza anthuwo.

Patapita zaka, Zedekiya anakhala mfumu ya Yuda. Koma ansembe ndi aneneri abodza ankadana ndi Yeremiya chifukwa cha uthenga umene ankalalikira. Iwo anauza akalonga kuti: ‘Munthu uyu akuyenera kuphedwa.’ Koma Yeremiya anati: ‘Mukandipha, ndiye kuti mwapha munthu wosalakwa. Ine ndimauza anthu mawu a Yehova osati anga.’ Akalongawo atamva zimenezi anati: ‘Munthu ameneyu sakuyenera kuphedwa.’

Yeremiya anapitiriza kulalikira ndipo akalongawo nawonso anakwiya naye kwambiri. Ndiyeno anapempha mfumu kuti Yeremiya aphedwe. Zedekiya anawauza kuti akhoza kumuchita Yeremiya chilichonse chimene angafune. Choncho iwo anamuponyera m’chitsime chakuya komanso chamatope kuti afere momwemo. Yeremiya anayamba kumira m’matopemo.

Kenako nduna ina ya mfumu dzina lake Ebedi-meleki anapita kukauza mfumu kuti: ‘Akalonga aja aponya Yeremiya m’chitsime. Tikamusiya momwemo ndiye kuti afa basi.’ Zedekiya anauza Ebedi-meleki kuti atenge anthu 30 ndipo apite kukamutulutsa. Ifenso tizitsanzira Yeremiya ndipo tisamalole chilichonse kuti chitilepheretse kulalikira.

“Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa, koma yekhayo amene adzapirire mpaka pa mapeto ndi amene adzapulumuke.”​—Mateyu 10:22