Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 57

Yehova Atumiza Yeremiya Kuti Akalalikile

Yehova Atumiza Yeremiya Kuti Akalalikile

Yehova anasankha Yeremiya kuti akhale mneneli kwa Ayuda. Anamuuza kuti akalalikile kwa anthu, na kuwacenjeza kuti aleke kucita zinthu zoipa. Koma Yeremiya anayankha kuti: ‘Yehova, ine ndine mwana. Sinidziŵa mokambila ndi anthu.’ Yehova anamuuza kuti: ‘Usacite mantha. Ine nidzakuuza zokakamba. N’dzakuthandiza.’

Yehova anauza Yeremiya kuti asonkhanitse akulu-akulu a mu mzinda, ndiyeno aphwanye mtsuko wamadzi pamaso pawo, na kuwauza kuti: ‘Umu ni mmenenso Yerusalemu adzam’phwanyila.’ Yeremiya atacita zimene Yehova anamuuza, akulu-akuluwo anakwiya kwambili. Ndipo wansembe wina, Pasuri, anamenya Yeremiya na kum’manga m’matangadza. Usiku wonse Yeremiya sanakwanitse kuyenda. Anam’masula m’mawa mwake. Cifukwa ca izi, Yeremiya anati: ‘Siningazikwanitse izi. N’dzaleka kulalikila.’ Koma kodi analeka? Iyai. Ataganizilapo anakamba kuti: ‘Uthenga wa Yehova uli monga moto mu mtima mwanga. Sinidzaleka kulalikila.’ Inde, Yeremiya anapitiliza kucenjeza anthu.

Zaka zinapitapo, ndipo Ayuda anakhala na mfumu yatsopano. Ansembe komanso aneneli onama anali kuipidwa nawo uthenga wa Yeremiya. Iwo anauza atsogoleli kuti: ‘Munthu uyu afunika kufa.’ Koma Yeremiya anati: ‘Ngati munganiphe, ndiye kuti mwapha munthu wosalakwa. Mawu amene nilankhula si anga, ni ocokela kwa Yehova.’ Atsogoleli atamva zimenezi anati: ‘Munthu uyu safunika kuphedwa.’

Koma pamene Yeremiya anapitiliza kulalikila, atsogoleli a anthu anakwiya kwambili. Anapempha mfumu kuti imuphe Yeremiya. Mfumu inawauza kuti angacite naye ciliconse cimene angafune. Iwo anatenga Yeremiya na kum’ponya m’citsime cakuya komanso ca matika kuti afe. Ndipo Yeremiya anayamba kumila m’matikamo.

Koma nduna ya pa nyumba ya mfumu dzina lake Ebedi-meleki, inauza mfumu kuti: ‘Akulu-akulu aponya Yeremiya m’citsime! Tikamusiya mmenemo adzafa.’ Mfumuyo inauza Ebedi-meleki kutenga amuna 30 kuti akacotse Yeremiya m’citsimemo. Kodi na ise sitiyenela kukhala monga Yeremiya, amene sanalole ciliconse kum’letsa kulalikila?

“Anthu onse adzadana nanu cifukwa ca dzina langa, koma yekhayo amene adzapilile mpaka pa mapeto ndi amene adzapulumuke.”—Mateyu 10:22