Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 58

Yerusalemu Awonongedwa

Yerusalemu Awonongedwa

Mobweleza-bweleza, Ayuda anamusiya Yehova na kuyamba kulambila milungu yonama. Yehova anayesa kuŵathandiza kwa zaka zambili. Anatuma aneneli ambili kuti aŵacenjeze, koma iwo sanali kumvela. M’malo mwake, anali kuŵaseka aneneliwo. Kodi Yehova anacitapo ciani kuti athetse kulambila mafano?

Nebukadinezara, mfumu ya ku Babulo, anali kugonjetsa mizinda umodzi-umodzi. Atagonjetsa mzinda wa Yerusalemu koyamba, anagwila Mfumu Yehoyakini, atsogoleli, asilikali, komanso amisili, na kuŵatenga kupita nawo ku Babulo. Anatenganso cuma conse ca m’kacisi wa Yehova. Kenako Nebukadinezara anasankha Zedekiya kukhala mfumu ya Yuda.

Poyamba, Zedekiya anali womvela kwa Nebukadinezara. Koma mitundu ina yapafupi, komanso aneneli onama anamusonkhezela kuti apandukile Ababulo. Koma Yeremiya anamucenjeza kuti: ‘Mukapandukila ulamulilo wa Babulo, anthu anu adzaphedwa, mu Yuda mudzakhala njala, komanso matenda.’

Atalamulila kwa zaka 8, Zedekiya anapandukila ufumu wa Babulo. Anapempha asilikali a ku Iguputo kuti am’thandize. Nebukadinezara anatumiza asilikali ake kuti akagonjetse Yerusalemu. Anapita na kumanga msasa mozungulila mzindawo. Yeremiya anauza Zedekiya kuti: ‘Yehova wakamba kuti ngati mudzagonjela Ababulo, mudzapulumuka pamodzi na mzinda wanu. Koma ngati simudzatelo, Ababulo adzashoka mzinda wa Yerusalemu, ndipo adzakutengani kuti mukakhale akaidi.’ Zedekiya anayankha kuti: ‘Siningayese kugonja!’

Patapita caka na hafu, Ababulo anagumula mpanda wa Yerusalemu na kushoka mzinda. Anashoka kacisi, kupha anthu ambili, komanso kutenga akaidi masauzande ambili.

Zedekiya anathaŵa mu mzinda wa Yerusalemu. Koma Ababulo anam’thamangitsa mpaka kukam’gwilila kufupi na mzinda wa Yeriko. Atam’peleka kwa Nebukadinezara mfumu ya Babulo, inapha ana a Zedekiya iye akuona. Kenako Nebukadinezara anam’boola maso Zedekiya, na kumuponya m’ndende mmene anafela pambuyo pake. Koma Yehova analonjeza Ayuda kuti: ‘Pambuyo pa zaka 70, nidzakubwezani ku Yerusalemu.’

Nanga zinakhala bwanji kwa acicepele amene anatengedwa kupita ku Babulo? Kodi anakhalabe okhulupilika kwa Yehova?

‘Yehova Mulungu, inu Wamphamvuzonse, zigamulo zanu n’zoona ndi zolungama.’—Chivumbulutso 16:7