Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 59

Anyamata Anayi Amene Anamvela Yehova

Anyamata Anayi Amene Anamvela Yehova

Pamene Nebukadinezara anatenga anyamata a m’mabanja acifumu ku Yuda kupita nawo ku Babulo, anaika nduna ya pa nyumba ya mfumu dzina lake Asipenazi, kukhala woyang’anila anyamatawo. Nebukadinezara anauza Asipenazi kuti pakati pa anyamata aciyudawo, asankhepo anyamata ang’ono-ang’ono athanzi labwino komanso anzelu kwambili. Anafuna kuti anyamata amenewo aŵaike pa maphunzilo kwa zaka zitatu. Colinga cinali cakuti akakhale nduna za ufumu wa Babulo. Anyamatawo anaphunzila kuŵelenga, kulemba, na kukamba citundu ca Ababulo. Anafunikanso kumadya zakudya zimene mfumu na onse a m’nyumba yake anali kudya. Anyamata anayi amene anasankhidwa anali Danieli, Hananiya, Misayeli na Azariya. Koma Asipenazi anawapatsa maina ena acibabulo akuti, Belitesazara, Sadirake, Mesake na Abedinego. Kodi iwo analeka kutumikila Yehova cifukwa ca maphunzilo amenewo?

Anyamata anayiwo sanaleke kumvela Yehova. Anadziŵa kuti safunikila kudya zakudya za mfumu, cifukwa zinaphatikizapo zakudya zoletsedwa m’Cilamulo ca Yehova. Conco anauza Asipenazi kuti: ‘Conde, musamatipatseko zakudya za mfumu.’ Asipenazi anati: ‘Mukakana kudya cakudyaco mudzayonda. Ndipo mfumu ikakuonani conco, ndithu idzanipha!’

Koma Danieli anadziŵa zocita. Iye anauza wowayang’anilayo kuti: ‘Conde, tiloleni kuti kwa masiku 10, tizidya zakudya zamasamba na kumwa madzi cabe. Kenako mukatiyelekeze na anyamata amene akudya zakudya za mfumu.’ Wowayang’anilayo anavomela.

Pambuyo pa masiku 10, Danieli na anzake atatu aja anali kuoneka athanzi kuposa anyamata ena onse. Yehova anakondwela nawo cifukwa anamumvela. Cakuti anapatsa Danieli nzelu zomvetsa masomphenya na maloto.

Maphunzilo atatha, Asipenazi anapeleka anyamatawo kwa Nebukadinezara. Mfumuyo pokamba nawo, inaona kuti Danieli, Hananiya, Misayeli na Azariya anali anzelu kwambili kupambana anyamata ena onse. Conco, anasankha anyamata anayi amenewa kuti azitumikila ku nyumba ya mfumu. Kaŵili-kaŵili, mfumu inali kufunsila uphungu kwa iwo pa nkhani zofunika kwambili. Yehova anawapatsa nzelu kwambili kupambana amuna anzelu a mfumu, ngakhalenso amatsenga ake.

Olo kuti anali m’dziko lacilendo, Danieli, Hananiya, Misayeli na Azariya sanaiŵale kuti anali anthu a Yehova. Kodi na iwe udzam’kumbukila Yehova nthawi zonse, ngakhale pamene uli kwa wekha kulibe makolo ako?

“Usalole kuti munthu aliyense akudelele poona kuti ndiwe wamng’ono. M’malomwake, ukhale citsanzo kwa okhulupilika m’kalankhulidwe, m’makhalidwe, m’cikondi, m’cikhulupililo, ndi pa khalidwe loyela.”—1 Timoteyo 4:12