Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 61

Anakana Kugwadila Fano

Anakana Kugwadila Fano

Patapita nthawi kucokela pamene Mfumu Nebukadinezara analota maloto a cifano cacikulu, anapanga cifano cacikulu cagolide. Anaciimika m’cigwa ca Dura, kenako anaitana akulu-akulu a boma, kuphatikizapo Sadirake, Mesake na Abedinego, kuti akasonkhane pamaso pa cifanoco. Kumeneko mfumu inalamula kuti: ‘Mukangomvela kulila kwa malipenga, zitolilo, azeze aang’ono, na zitolilo zathumba, mugwade na kuŵelamila fano ili! Aliyense amene sadzacita zimenezi, adzaponyedwa mu ng’anjo yoyaka moto.’ Kodi Aheberi atatu anagwadila fanolo, kapena anakhalabe okhulupilika kwa Yehova?

Ndiyeno mfumu inalamula kuti zoimbilazo zilile. Pamenepo aliyense anagwada pansi na kulambila fano limenelo, kusiyapo cabe Sadirake, Mesake na Abedinego. Koma anthu ena anawaona, ndipo anauza mfumu kuti: ‘Aheberi atatu aja akana kulambila fano lanu.’ Nebukadinezara anaitanitsa Aheberi aja n’kuwauza kuti: ‘Nikupatsani mwayi wina wakuti mulambile fano limeneli. Ngati mukana, nikuponyani mu ng’anjo ya moto. Ndipo palibe mulungu ati akupulumutseni kwa ine.’ Poyankha iwo anati: ‘Sitifuna mwayi wina. Mulungu wathu adzatipulumutsa. Koma ngakhale asatipulumutse, dziŵani mfumu, kuti zolambila fano ili sitingacite.’

Nebukadinezara anakalipa kwambili. Ndipo anauza atumiki ake kuti: ‘Sonkhezani moto kuwilikiza ka 7 kuposa mwa nthawi zonse!’ Ndiyeno anauza asilikali ake kuti: ‘Amangeni, muŵaponye mmenemo!’ Ng’anjo inatentha maningi, cakuti kungoiyandikila cabe asilikaliwo anafa. Aheberi atatu aja anagwela mu ng’anjo ya motoyo. Koma Nebukadinezara posonjola mkati mwa ng’anjoyo, anaona kuti muli anthu anayi akuyenda-yenda, m’malo mwa anthu atatu. Anacita mantha kwambili, ndipo anauza nduna zake kuti: ‘Kodi sitinaponyemo anthu atatu mu ng’anjo? Koma nionamo anayi, ndipo mmodzi wa iwo aoneka monga mngelo!’

Nebukadinezara anayenda pafupi na ng’anjoyo na kufuula kuti: ‘Tulukani inu atumiki a Mulungu Wakumwambamwamba!’ Anthu onse anadabwa poona Sadirake, Mesake na Abedinego akutuluka ali bwino-bwino. Khungu lawo, tsitsi lawo, komanso zovala zawo sizinapse ayi. Sananunkhe ngakhale fungo la moto.

Nebukadinezara anati: ‘Mulungu wa Sadirake, Mesake na Abedinego ni wamphamvu zoona. Watumiza mngelo wake kuti awapulumutse. Palibe mulungu wina angalingane naye.’

Monga Aheberi atatu aja, kodi ndiwe wokonzeka kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova, olo zinthu zivute bwanji?

“Yehova Mulungu wako ndi amene uyenela kumulambila, ndipo uyenela kutumikila iye yekha basi.” —Mateyu 4:10