Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZIIO 62

Ufumu Umene Uli Monga Mtengo Waukulu

Ufumu Umene Uli Monga Mtengo Waukulu

Tsiku lina usiku, Nebukadinezara analota maloto ocititsa mantha. Anaitana amuna anzelu kuti amuuze tanthauzo la zimene analota. Koma palibe amene anakwanitsa kumasulila malotowo. Pothela pake, mfumuyo inaitana Danieli.

Nebukadinezara anauza Danieli kuti: ‘Mu maloto anga, naona mtengo umene unakula mpaka pamwamba kwambili. Unali kuoneka kulikonse pa dziko lapansi. Unali na masamba okongola na zipatso zambili. Nyama zinali kupumula mu mthunzi wake, ndipo mbalame zinali kumanga zisa m’nthambi zake. Kenako, mngelo anatsika kucokela kumwamba. Iye anafuula kuti: “Gwetsani mtengowo, ndipo dulani nthambi zake. Koma musiye citsa cake na mizu yake m’nthaka. Citsaco mucimange na mikombelo, wina wacitsulo ndipo wina wamkuwa. Mtima wa mtengowo udzasintha kucoka pa mtima wa munthu n’kukhala mtima wa nyama, mpaka patapita nthawi 7. Anthu onse adzadziŵa kuti Mulungu ndiye Wolamulila, ndi kuti angapeleke ufumu kwa aliyense amene afuna kum’patsa.”’

Yehova anauza Danieli tanthauzo la malotowo. Pamene Danieli anadziŵa tanthauzo la malotowo, anacita mantha. Iye anati: ‘Pepani mfumu, nikanakonda cikanakhala kuti malotowa akukhudza adani anu, koma akamba za imwe. Mtengo waukulu umene unaduliwa ndimwe. Mudzasiya ufumu wanu, ndipo mudzadya udzu monga nyama yakuthengo. Koma cifukwa mngelo anati asacotse citsa na mizu yake, mudzakhalanso mfumu.’

Patapita caka, Nebukadinezara anali kuyenda pa mtenje wafulati wa nyumba yake yacifumu. Anali kuyang’ana kukongola kwa mzinda wa Babulo. Iye anati: ‘Onani kukongola mzinda umene n’namanga. Onani ulemelelo wanga!’ Mawu akali m’kamwa, kumwamba kunamveka mawu akuti: ‘Nebukadinezara! Tsopano ufumu wacoka m’manja mwako.’

Pamenepo Nebukadinezara anafuntha n’kukhala monga nyama yakuthengo. Anthu anam’cotsa mu nyumba yake yacifumu, cakuti anapita kukakhala na nyama msanga kapena kuti kuthengo. Tsitsi la Nebukadinezara linatalimpha monga nthenga za ciwombankhanga. Ndipo zikhadabo zake zinatalimpha monga za mbalame.

Patapita zaka 7, Nebukadinezara anakhalanso munthu wabwino-bwino, ndipo Yehova anam’bwezelanso pa ufumu wa Babulo. Pamenepo Nebukadinezara anati: ‘Nitamanda Yehova, Mfumu ya kumiyamba. Lomba nadziŵa kuti Yehova ndiye Wolamulila. Amatsitsa anthu onyada, ndipo angapeleke ufumu kwa aliyense amene afuna kum’patsa.’

“Kunyada kumafikitsa munthu ku ciwonongeko, ndipo mtima wodzikuza umacititsa munthu kupunthwa.”—Miyambo 16:18