Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 65

Mfumukazi Esitere Apulumutsa Anthu a Mtundu Wake

Mfumukazi Esitere Apulumutsa Anthu a Mtundu Wake

Esitere anali mtsikana waciyuda, ndipo anali kukhala ku Perisiya mu mzinda wa Susani. Zaka zambili kumbuyoko, banja la kwawo linatengedwa ku Yerusalemu, mwa lamulo la Nebukadinezara. Esitere analeledwa na wacibale wake Moredekai, amene anali mtumiki wa Ahasiwero, Mfumu ya Perisiya.

Mfumu Ahasiwero anali kufuna mkazi watsopano. Atumiki ake anam’bweletsela atsikana okongola kwambili a m’dzikolo, kuphatikizaponso Esitere. Pa atsikana onsewo, mfumu inasankhapo Esitere kukhala mkazi wake, kapena kuti mfumukazi. Moredekai anauza Esitere kuti asakaulule kuti ni Myuda.

Mwamuna wina wonyada, dzina lake Hamani, ndiye anali mkulu wa nduna zonse. Iye anali kufuna kuti aliyense azim’gwadila. Koma Moredekai anakana kucita zimenezo. Hamani anakalipa kwambili cakuti anaganiza za kumupha. Hamani atadziŵa kuti Moredekai anali Myuda, anapanga pulani yakuti Ayuda onse m’dzikolo aphedwe. Conco anauza mfumu kuti: ‘Ayuda ni anthu osamvela malamulo, afunika muwaphe.’ Ahasiwero anati: ‘Cita nawo ciliconse cimene ufuna,’ ndipo anam’patsa mphamvu yopanga lamulo. Hamani anapanga lamulo lakuti pa 13 m’mwezi wa Adara, anthu afunika kuti akaphe Ayuda onse. Koma Yehova anali kuyang’ana.

Esitere sanadziŵe za lamulo limenelo. Conco Moredekai anatumizila Esitere kope ya kalatayo, na kumuuza kuti: ‘Pita ukakambe na mfumu.’ Koma Esitere anati: ‘Aliyense wopita kwa mfumu cosaitanidwa amaphedwa. Mfumu siinaniitane kwa masiku 30 tsopano! Koma nipitabe. Ngati mfumu idzanilata na ndodo yake, nidzakhala na moyo. Koma ikapanda kutelo, nidzaphedwa.’

Esitere anapita ku bwalo la mfumu. Mfumu itamuona, inamulata na ndodo yake. Atayandikila kwa mfumu, inamufunsa kuti: ‘Ufuna nikucitile ciani Esitere?’ Iye anati: ‘Nipempha kuti mubwele kuphwando pamodzi na Hamani.’ Ali kuphwando kumeneko, Esitere anaŵaitanilanso kuphwando lina pa tsiku lokonkhapo. Pa phwando laciŵililo, mfumu inafunsanso Esitere kuti: ‘Ufuna nikucitile ciani?’ Esitere anati: ‘Munthu wina afuna kupha ine na mtundu wanga wonse. Conde tipulumutseni.’ Mfumu inafunsa kuti: ‘Ndani afuna kukupha?’ Iye anati: ‘Munthu woipayo ni uyu Hamani.’ Ahasiwero anakalipa kwambili, cakuti analamula kuti Hamani aphedwe nthawi yomweyo.

Koma palibe amene akanasintha lamulo la Hamani, ngakhale mfumu imene. Conco, mfumu inasankha Moredekai kukhala mkulu wa nduna zonse, na kum’patsa mphamvu zakuti apange lamulo latsopano. Moredekai anapanga lamulo lakuti Ayuda afunika kudziteteza adani awo powaukila. Pa tsiku la 13 m’mwezi wa Adara, Ayuda anagonjetsa adani awo onse. Kucokela pa tsiku limenelo, Ayuda anali kukondwelela cipambano cimeneci caka ciliconse.

“Adzakutengelani kwa abwanamkubwa ndi mafumu cifukwa ca ine, kuti ukhale umboni kwa iwo ndi kwa anthu a mitundu ina.”—Mateyu 10:18