Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 66

Ezara Aphunzitsa Cilamulo ca Mulungu

Ezara Aphunzitsa Cilamulo ca Mulungu

Aisiraeli ambili anali atabwelela ku Yerusalemu, ndipo panapita zaka pafupi-fupi 70. Koma ena anali kukhalabe m’madela osiyana-siyana a Ufumu wa Perisiya. Ndipo mmodzi wa iwo anali Ezara, amene anali kuphunzitsa Cilamulo ca Yehova. Ezara anamvela kuti anthu ku Yerusalemu sanali kutsatila Cilamulo, conco anafuna kupita kuti akawathandize. Aritasasita, Mfumu ya Perisiya, anamuuza kuti: ‘Mulungu anakupatsa nzelu kuti uziphunzitsa Cilamulo cake. Pita, tenga aliyense amene afuna kupita nawe.’ Ezara anakumana na onse ofuna kubwelela ku Yerusalemu. Iwo anapemphela kwa Yehova kuti awateteze pa ulendo wawo, kenako anauyamba ulendo.

Anayenda kwa miyezi 4 kuti akafike ku Yerusalemu. Kumeneko, atsogoleli anauza Ezara kuti: ‘Aisiraeli analeka kumvela Yehova, ndipo akukwatila akazi olambila milungu yonama.’ Kodi Ezara anacita bwanji? Pamaso pa anthu, Ezara anagwada pansi na kuyamba kupemphela kuti: ‘Yehova, mwaticitila zambili, koma takucimwilani.’ Ngakhale kuti anthuwo analapa, sanalekeletu kucita zinthu zoipa. Conco, Ezara anasankha akulu na oweluza kuti acitepo kanthu. Patapita miyezi itatu, onse amene sanali kulambila Yehova anawathamangitsa.

Zaka 12 zinapita. Pa nthawiyo, mpanda wa Yerusalemu unamangidwanso. Conco, Ezara anasonkhanitsa anthu kuti awaŵelengele Cilamulo ca Mulungu. Ezara atatsegula buku la Cilamulo, anthuwo anaimilila. Iye anatamanda Yehova, ndipo anthu nawonso anakweza manja awo kuvomeleza. Kenako Ezara anaŵelenga na kufotokozela Cilamulo, ndipo anthu anali kumvetsela mwachelu. Iwo anavomeleza kuti anali atapatukanso kwa Yehova, ndipo anayamba kulila. Tsiku lotsatila, Ezara anapitiliza kuwaŵelengela Cilamulo. Anthu anadziŵa kuti posacedwa adzafunika kucita Cikondwelelo ca Misasa. Nthawi yomweyo anayamba kukonzekela cikondweleloco.

Pa masiku 7 a cikondwelelo, anthuwo anasangalala, na kuyamikila Yehova cifukwa ca zokolola zambili. Kucokela m’masiku a Yoswa, sipanacitekepo Cikondwelelo ca Misasa kuposa cimeneco. Pambuyo pa cikondwelelo, anthu anasonkhana n’kupemphela kuti: ‘Yehova, munatipulumutsa kuukapolo, munatipatsa cakudya m’cipululu, komanso munatipatsa dziko lokongola. Koma ise takhala tikukupandukilani mobweleza-bweleza. Munatitumizila aneneli kuti aticenjeze, koma ife sitinawamvelele. Koma inu munatilezelabe mtima. Munasunga lonjezo lanu kwa Abulahamu. Koma lomba, tilonjeza kuti tidzakumvelani.’ Anacita kulemba lonjezo lawo, ndipo atsogoleli, Alevi, komanso ansembe anatsimikizila za lonjezolo mwa kuikapo cisindikizo cawo.

“Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!” —Luka 11:28