Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 67

Mpanda wa Yerusalemu Umangidwanso

Mpanda wa Yerusalemu Umangidwanso

M’nthawi ya Ezara, kunalinso mwiisiraeli wina dzina lake Nehemiya, amene anali mtumiki wa Mfumu Aritasasita. Anali kukhala mumzinda wa Perisiya ku Susani. M’bale wake wa Nehemiya anabwela kucokela ku Yuda na uthenga woipa. Iye anati: ‘Anthu amene anabwelela ku Yerusalemu ali pa ciwopsezo. Mpanda wa mzinda komanso zipata zake zimene Ababulo anawononga zikalibe kumangidwanso.’ Nehemiya atamva izi anakhumudwa kwambili. Iye anaganiza zopita ku Yerusalemu kuti akathandize. Conco, anapemphela kuti mfumu imulole kuti akapite.

Patapita nthawi, mfumu inaona kuti Nehemiya anali kuoneka wacisoni. Conco inam’funsa kuti: ‘Sin’nakuonepo wacisoni conco. Cavuta n’ciani?’ Nehemiya anati: ‘N’lekelenji kukhala wacisoni, mzinda wathu wa Yerusalemu ukali matongwe.’ Mfumu inafunsa kuti: ‘Ufuna nikucitile ciani?’ Pamenepo Nehemiya anapemphela ca mu mtima. Kenako anati: ‘Conde, niloleni nipite ku Yerusalemu nikamange mpanda.’ Mfumu inalola Nehemiya kupita, ndipo inacita zonse zotheka kuti akatetezeke pa ulendo wake. Anamuikanso Nehemiya kukakhala bwanamkubwa wa ku Yuda, na kum’patsanso mapulanga okapangila mageti a mzindawo.

Nehemiya atafika ku Yerusalemu, anayendela mpanda wa mzinda. Kenako anasonkhanitsa ansembe komanso atsogoleli onse, na kuwauza kuti: ‘Zinthu sizili bwino. Tiyeni tiiyambe nchito.’ Anthu onse anavomeleza, ndipo anayamba kumanganso mpanda.

Koma adani ena a Aisiraeli anayamba kuwaseka, amvekele: ‘Ngakhale nkhandwe ikhoza kugwetsa mpanda umene mukumangawu.’ Aisiraeli anangonyalanyaza manyozowo na kupitiliza nchito yawo. Mpandawo unakwelela-kwelela na kulimbila-limbila.

Adaniwo anaganiza zoukila Yerusalemu modzidzimutsa, ndipo anabwela kucokela ku mbali zosiyana-siyana. Ayuda atamva zimenezi, anacita mantha kwambili. Koma Nehemiya anawauza kuti: ‘Musacite mantha. Yehova ali na ife.’ Iye anaika alonda kuti ateteze omangawo, cakuti adaniwo sanakwanitse kuŵaukila.

M’masiku 52 cabe, mpandawo unatha na zipata zake zonse. Kenako, Nehemiya anamemeza Alevi onse, kapena kuti kuŵaitanila ku Yerusalemu ku mwambo wopatulila mpanda. Anaŵagawa m’magulu aŵili oimba. Iwo anakwela pamwamba pa mpanda mwa kuseŵenzetsa masitepu a pa Cipata ca Kumadzi. Gulu lina linaloŵela mbali ya uku, linanso n’kuloŵela mbali ya uku n’kumazungulila mzinda. Analiza malipenga, zinganga, komanso azeze, akumaimbila Yehova. Ezara anapita na gulu limodzi, pamene Nehemiya nayenso anapita na gulu lina, mpaka anakumana ku kacisi. Anthu onse, amuna, akazi, ngakhale ana, anapeleka nsembe kwa Yehova, na kucita cikondwelelo. Cisangalalo cawo cinali kumveka mpaka malo akutali kwambili.

“Cida ciliconse cimene cidzapangidwe kuti cikuvulaze sicidzapambana.”—Yesaya 54:17