Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 68

Elizabeti Anakhala ndi Mwana

Elizabeti Anakhala ndi Mwana

Patatha zaka zoposa 400 kuchokera pamene mpanda wa Yerusalemu unakonzedwa, wansembe wina ankakhala pafupi ndi mzinda wa Yerusalemu. Dzina lake anali Zekariya ndipo mkazi wake anali Elizabeti. Iwo anakhala m’banja zaka zambiri koma analibe mwana. Tsiku lina Zekariya akupereka nsembe m’nyumba yopatulika, anaona mngelo Gabirieli. Zekariya anaopa kwambiri, koma Gabirieli anamuuza kuti: ‘Usaope. Ndakubweretsera uthenga wabwino wochokera kwa Yehova. Mkazi wako adzakhala ndi mwana ndipo dzina lake lidzakhala Yohane. Yehova akufuna kuti Yohaneyo adzagwire ntchito yapadera.’ Zekariya anafunsa kuti: ‘Ndingakhulupirire bwanji zimene mukunenazi? Ine ndi mkazi wanga ndife okalamba ndipo n’zosatheka kukhala ndi mwana.’ Gabirieli anati: ‘Mulungu ndi amene wandituma kuti ndidzakuuze zimenezi. Koma poti sukukhulupirira, ukhala wosalankhula mpaka mwanayo adzabadwe.’

Zekariya anakhala m’nyumba yopatulikayo kwa nthawi yaitali. Ndiyeno atatuluka, anthu ankafuna kudziwa chimene chinamuchedwetsa. Koma Zekariya sankatha kulankhula. Ndiyeno anangoyamba kulankhula pogwiritsa ntchito manja. Anthuwo anazindikira kuti iye walandira uthenga wochokera kwa Mulungu.

Patapita nthawi, zimene mngelo uja ananena zinachitikadi. Elizabeti anakhala woyembekezera ndipo kenako anabereka mwana wamwamuna. Anzake a Elizabeti komanso achibale ake anabwera kudzaona mwanayo ndipo anasangalala kwambiri. Ndiyeno Elizabeti anawauza kuti: ‘Dzina la mwanayu ndi Yohane.’ Anthuwo anati: ‘Koma m’banja lanu mulibe aliyense amene ali ndi dzina limeneli. Bwanji atenge dzina la bambo ake lakuti Zekariya?’ Zitatero, Zekariya analemba kuti: ‘Dzina lake ndi Yohane.’ Atangolemba zimenezi, anayamba kulankhula. Nkhani ya mwanayu inafalikira mu Yudeya monse ndipo anthu ankadabwa kuti: ‘Kodi mwana ameneyu adzakhala wotani akadzakula?’

Zekariya anadzazidwa ndi mzimu woyera. Ndiyeno ananena kuti: ‘Yehova atamandike. Analonjeza Abulahamu kuti adzatumiza Mesiya kuti atipulumutse. Yohane adzakhala mneneri ndipo adzakonza njira ya Mesiya.’

Pa nthawi yomweyi, zinthu zina zochititsa chidwi zinachitikiranso m’bale wake wa Elisabeti, dzina lake Mariya. M’mutu wotsatira tikambirana nkhani yake.

“Kwa anthu zimenezi n’zosathekadi, koma zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.”​—Mateyu 19:26