Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 68

Elizabeti Akhala na Mwana

Elizabeti Akhala na Mwana

Patapita zaka 400 kucokela pamene mpanda wa Yerusalemu unamangidwanso, wansembe wina dzina lake Zakariya na mkazi wake Elizabeti, anali kukhala pafupi na mzinda wa Yerusalemu. Anakhala m’cikwati kwa zaka zambili, koma analibe ana. Tsiku lina pamene Zakariya anali kufukiza nsembe mu kacisi, mngelo Gabirieli anaonekela kwa iye. Zakariya anacita mantha kwambili, koma Gabirieli anati: ‘Usacite mantha. Nakubweletsela uthenga wabwino wocokela kwa Yehova. Mkazi wako Elizabeti adzabala mwana wamwamuna, ndipo dzina lake adzakhala Yohane. Yehova wasankhilatu Yohane kuti akagwile nchito yapadela.’ Koma Zakariya anafunsa kuti: ‘Nidzakhulupilila bwanji zimenezi? Ine na mkazi wanga ndise okalamba moti sitingabale mwana.’ Gabirieli anati: ‘Mulungu ndiye wanituma kuti nidzakuuze uthengawu. Koma cifukwa sunanikhulupilile, udzaleka kukamba mpaka mwanayo akabadwe.’

Zakariya anacedwamo m’kacisi kuposa masiku onse. Conco atatuluka, anthu omuyembekezela panja anafuna kudziŵa kuti cinam’cedwetsa n’ciani. Koma Zakariya anali ataleka kukamba. Anali kukamba na manja cabe. Pamenepo anthu anadziŵa kuti walandila uthenga wocokela kwa Mulungu.

M’kupita kwa nthawi, Elizabeti anakhala na pakati, ndipo anabala mwana wamwamuna, monga mmene mngelo anakambila. Anzake ndi abululu ake anabwela kudzaona mwanayo, ndipo anakondwela kwambili. Ndiyeno Elizabeti anati: ‘Dzina lake adzakhala Yohane.’ Koma iwo anati: ‘Palibe ali na dzina lakuti Yohane m’banja mwanu. M’patseni dzina la atate ake lakuti Zakariya.’ Koma Zakariya analemba mawu akuti: ‘Dzina lake ni Yohane.’ Pamenepo Zakariya anayambanso kukamba! Mbili ya mwanayo inafalikila mu Yudeya monse, ndipo anthu anali kufunsa kuti: ‘Kodi mwana ameneyu adzakhala munthu wotani akadzakula?’

Pamenepo Zakariya anadzazidwa na mzimu woyela. Kenako analosela kuti: ‘Yehova atamandike. Iye analonjeza Abulahamu kuti adzatumiza mpulumutsi, amene ni Mesiya, kuti akatipulumutse. Yohane adzakhala mneneli, ndipo adzakonzela njila Mesiya.’

Komanso, cina cake capadela cinacitika kwa Mariya, m’bululu wa Elizabeti. Tidzamvela zambili m’nkhani yotsatila.

“Kwa anthu zimenezi n’zosathekadi, koma zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.”?—Mateyu 19:26