Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 70

Angelo Analengeza za Kubadwa kwa Yesu

Angelo Analengeza za Kubadwa kwa Yesu

Kaisara Augusto, Wolamulila mu Ufumu wa Roma, analamula Ayuda onse kuti abwelele ku matauni akwawo kuti akadzilembetse m’kaundula. Conco, Yosefe na Mariya anapita ku Betelehemu, kwawo kwa Yosefe. Ndipo masiku anayandikila akuti Mariya abale mwana.

Atafika ku Betelehemu, anapeza kuti nyumba zonse n’zodzala. Conco anagona m’khola la ziŵeto. Mmenemo ndiye mmene Mariya anabalila mwana wake wamwamuna, dzina lake Yesu. Anamuika m’nsalu zofeŵa bwino, na kum’goneka bwino-bwino m’codyelamo ziŵeto.

Pafupi na Betelehemu, panali aciŵeta amene anali kuyang’anila ziŵeto zawo usiku. Mwadzidzidzi, mngelo anaima pafupi nawo, ndipo ulemelelo wa Yehova unawawalila. Aciŵetawo anacita mantha kwambili, koma mngelo anati: ‘Musaope. Ndili na uthenga wokondweletsa. Mesiya wabadwa lelo ku Betelehemu.’ Pa nthawi imeneyo, angelo ambili anaonekela m’mwamba, ndipo anali kufuula kuti: ‘Ulemelelo kwa Mulungu wakumwamba-mwamba, na mtendele pa dziko lapansi.’ Kenako angelowo anasoŵa. Kodi abusawo anacita bwanji?

Iwo anayamba kuuzana kuti: ‘Tiyeni tipite ku Betelehemu.’ Anapita mwamsanga-msanga, ndipo anapeza kuti Yosefe na Mariya ali m’khola, na mwana wawo wakhanda.

Aliyense amene anamvela zimene mngelo anauza abusa aja anadabwa. Mariya anaganizilapo kwambili pa mawu amene mngelo anakamba, ndipo sanawaiŵale. Abusa aja anabwelela kukayang’anila ziŵeto zawo, ndipo anayamikila Yehova pa zonse zimene anaona na kumva.

“Ine ndinacokela kwa Mulungu ndipo ndili pano. Sindinabwele mwakufuna kwanga ayi, koma Iyeyo anandituma.”—Yohane 8:42