Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 71

Yehova Anateteza Yesu

Yehova Anateteza Yesu

M’dziko lina lakum’mawa kwa Isiraeli, kunali anthu amene ankakhulupirira kuti nyenyezi zingawathandize kudziwa zinthu. Tsiku lina, anthu ena ochokera kudzikoli anaona chinthu chokhala ngati nyenyezi chikuyenda m’mwamba ndipo anayamba kuchitsatira. Iwo anachitsatira mpaka kukafika ku Yerusalemu. Atafika anayamba kufunsa anthu kuti: ‘Kodi mwana amene adzakhale mfumu ya Ayuda ali kuti? Tabwera kuti tidzamugwadire.’

Herode atamva zimenezi anada nkhawa. Iye anafunsa ansembe aakulu kuti: ‘Paja mfumu imeneyi iyenera kubadwira kuti?’ Ansembewo anamuyankha kuti: ‘Aneneri ananena kuti ku Betelehemu.’ Ndiyeno Herode anauza anthu ochokera kum’mawawo kuti: ‘Pitani ku Betelehemu mukafufuze mwanayo. Mukakamupeza mubwere mudzandiuze. Nanenso ndikufuna ndikamugwadire.’ Koma sikuti Herode ankafunadi kuti akamugwadire mwanayo.

Chinthu chokhala ngati nyenyezi chija chinayambanso kuyenda ndipo anthu aja anapitiriza kuchitsatira. Ndiyeno chinakaima panyumba inayake. Atalowa m’nyumbayo anapeza Yesu ndi amayi ake. Iwo anaweramira mwanayo ndipo anapereka mphatso za golide, lubani ndi mule. Komatu si Yehova amene anatuma anthuwa kuti akaone Yesu.

Usiku womwewo, Yehova analankhula ndi Yosefe m’maloto. Anamuuza kuti: ‘Herode akufuna kupha Yesu. Tenga mkazi wako ndi mwanayo ndipo muthawire ku Iguputo. Mukakhale komweko mpaka nthawi imene ndidzakuuzeni kuti mubwerere.’ Nthawi yomweyo, Yosefe ananyamuka ndi banja lake kupita ku Iguputo.

Ndiyeno Yehova anauza anthu ochokera kum’mawa aja kuti asadzere kwa Herode. Herodeyo atazindikira zoti anthuwo adutsa njira ina, anakwiya kwambiri. Popeza zinali zovuta kuti apeze Yesu, analamula kuti ana aamuna amsinkhu wa Yesu ku Betelehemu aphedwe. Pamene izi zinkachitika, n’kuti Yesu ali ku Iguputo.

Patapita nthawi, Herode anafa. Ndiyeno Yehova anauza Yosefe kuti: ‘Tsopano ukhoza kubwerera.’ Yosefe, Mariya ndi Yesu anabwerera ku Isiraeli ndipo anakafikira ku Nazareti.

“Ndi mmenenso adzakhalire mawu otuluka pakamwa panga. . . . Adzakwaniritsadi zimene ndinawatumizira.”​—Yesaya 55:11