Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 71

Yehova Anam’teteza Yesu

Yehova Anam’teteza Yesu

Kudziko la kum’maŵa kwa Isiraeli, kunali anthu okhulupilila kuti nyenyezi zingawathandize kudziŵa zinthu. Tsiku lina usiku, amuna ena a Kum’maŵako anaona “nyenyezi” ina kumwamba ikuyenda, ndipo anayamba kuitsatila. “Nyenyezi” imeneyo inaŵatsogolela ku Yerusalemu. Kumeneko amunawo anafunsa anthu kuti: ‘Ali kuti mwana amene adzakhala mfumu ya Ayuda? Tabwela kudzam’gwadila.’

Koma Herode, mfumu ya ku Yerusalemu atamvela kuti kwabadwa mfumu yatsopano, anada nkhawa kwambili. Anafunsa ansembe aakulu kuti: ‘Kodi mfumu imeneyi yabadwila kuti?’ Iwo anamuuza kuti: ‘Aneneli anakamba kuti adzabadwila ku Betelehemu.’ Conco, Herode anaitana amuna a Kum’maŵa aja na kuŵauza kuti: ‘Pitani ku Betelehemu mukafunefune mwana ameneyu. Mukakam’peza, mudzaniuze kumene alili. Inenso nifuna nikam’gwadile.’ Koma anali kunama.

“Nyenyezi” ija inayambanso kuyenda, ndipo amuna aja anapitiliza kuikonkha kuloŵela ku Betelehemu. “Nyenyeziyo” inaima pamwamba pa nyumba inayake, ndipo amunawo analoŵa m’nyumbayo. Anapeza Yesu, na mayi wake Mariya. Iwo anam’gwadila mwanayo, na kum’patsa mphatso za golide, lubani (mafuta onunkhila ofukiza), komanso mafuta a mule. Kodi Yehova ndiye anatuma amuna amenewa kuti akafune-fune Yesu? Iyai.

Tsiku limenelo usiku, Yehova anauza Yosefe m’maloto kuti: ‘Herode afuna kupha Yesu. Tenga mkazi wako na mwanayu uthaŵile ku Iguputo. Ukakhale kumeneko mpaka n’kakuuze kuti ubwelele.’ Nthawi yomweyo, Yosefe na banja lake ananyamuka kupita ku Iguputo.

Yehova anauza amuna a Kum’maŵa kuti asabwelele kwa Herode. Pamene Herode anadziŵa kuti amuna aja sadzabwelanso, anakwiya kwambili. Cifukwa colephela kupeza Yesu, analamula kuti ana onse aamuna a msinkhu monga wa Yesu, aphedwe mu Betelehemu. Koma Yesu anali wotetezeka kutali ku Iguputo.

M’kupita kwa nthawi, Herode anamwalila. Ndiyeno Yehova anauza Yosefe kuti: ‘Ungabwelele lomba.’ Yosefe, Mariya, komanso Yesu anabwelela ku Isiraeli, ndipo anapita kukakhala mu mzinda wa Nazareti.

“Ndi mmenenso adzakhalile mawu otuluka pakamwa panga . . . , adzakwanilitsadi zimene ndinawatumizila.”—Yesaya 55:11