Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 72

Zimene Yesu Anachita Ali Wamng’ono

Zimene Yesu Anachita Ali Wamng’ono

Yosefe ndi Mariya ankakhala ku Nazareti. Ankakhala limodzi ndi Yesu komanso ana awo ena aamuna ndi aakazi. Yosefe ankagwira ntchito ya ukalipentala kuti azipeza ndalama zothandizira banja lake. Iye ankaphunzitsanso banja lakelo za Yehova komanso Chilamulo chake. Yosefe ndi banja lake ankapita kusunagoge kukalambira Yehova nthawi zonse. Komanso chaka chilichonse banjali linkayenda ulendo wautali wopita ku Yerusalemu kukachita nawo chikondwerero cha Pasika.

Yesu ali ndi zaka 12, banja lawo linapitanso ku Yerusalemu monga linkachitira zaka zonse. Ku Yerusalemuko kunali anthu ambirimbiri amene anabwera kudzachitanso chikondwerero cha Pasika. Chikondwererochi chitatha Yosefe ndi Mariya komanso anthu ena anayamba ulendo wobwerera kunyumba. Iwo ankaganiza kuti Yesu ali nawo limodzi. Koma kenako anazindikira kuti Yesu palibe. Anamuyang’ana pakati pa achibale onse koma sanamupeze.

Yosefe ndi Mariya anabwereranso ku Yerusalemu ndipo anamufufuza kwa masiku atatu koma sanamupeze. Iwo anada nkhawa kwambiri ndi zimenezi. Kenako anapita kukamuyang’ana m’kachisi. Anamupeza ali ndi aphunzitsi angapo ndipo ankamvetsera zimene iwo ankanena komanso ankawafunsa mafunso. Aphunzitsiwo ankachita chidwi kwambiri ndi Yesu moti nawonso ankamufunsa mafunso. Koma ankadabwa ndi mmene iye ankawayankhira. Anazindikira kuti Yesu ankachidziwa bwino Chilamulo cha Yehova.

Yosefe ndi Mariya ataona Yesu, Mariya anamufunsa kuti: ‘Takhala tikukufufuza kwa nthawi yaitali. Unali kuti?’ Koma Yesu anayankha kuti: ‘Kodi simukudziwa kuti ndiyenera kupezeka m’nyumba ya Atate wanga?’

Yesu ananyamuka ndi makolo akewo n’kumapita ku Nazareti. Yosefe anaphunzitsa Yesu ntchito ya ukalipentala. Kodi ukuganiza kuti Yesu ali wamng’ono anali munthu wotani? Pamene iye ankakula nzeru zakenso zinkawonjezeka ndipo ankakondedwa ndi Mulungu komanso anthu.

“Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga, ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.”​—Salimo 40:8