Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 73

Yohane Anakonza Njila

Yohane Anakonza Njila

Yohane, mwana wa Zekariya na Elizabeti, atakula anakhala mneneli. Monga mneneli, Yehova anam’seŵenzetsa kuphunzitsa anthu kuti Mesiya adzabwela. M’malo mophunzitsa anthu m’masunagoge na m’matauni, Yohane anali kulalikila ku cipululu. Conco, anthu anali kubwela kwa iye kucokela ku Yerusalemu na ku madela onse a ku Yudeya. Anali kubwela kuti iye awaphunzitse. Powaphunzitsa, anali kuwauza kuti ngati afuna kukondweletsa Mulungu, afunika kuleka kucita zoipa. Atamvetsela zimene Yohane anali kuwauza, ambili analapa, ndipo Yohane anawabatiza mu Mtsinje wa Yorodano.

Yohane anali na umoyo wosalila zambili. Anali kuvala covala caubweya wa ngamila. Cakudya cake cinali dzombe na uci. Anthu anali kucita naye cidwi Yohane. Ngakhale Afarisi na Asaduki onyada aja anabwela kudzamuona. Yohane atawaona, anawauza kuti: ‘Lekani khalidwe loipa, ndipo lapani. Musaganize kuti ndimwe anthu apadela, cabe cifukwa mumati ndimwe ana a Abulahamu. Koma sikuti ndimwe ana a Mulungu iyai.’

Ayuda ambili atamvela zimenezi, anam’funsa Yohane kuti: ‘Nanga tingacite ciani kuti tim’kondweletse Mulungu?’ Yohane anawayankha kuti: ‘Ngati muli na zovala ziŵili, cimodzi mupatseko amene alibe.’ Udziŵa cimene anakambila zimenezi? Anafuna kuti iwo adziŵe kuti ngati afuna kukondweletsa Mulungu, afunika kukonda anthu anzawo.

Yohane anauza okhometsa msonkho kuti: ‘Muzicita zinthu moona mtima. Musamacite zacinyengo kwa aliyense.’ Kwa asilikali, anati: ‘Musamalandile ziphuphu kapena kunama bodza.’

Nawonso Ansembe na Alevi anabwela kwa Yohane. Anam’funsa kuti: ‘Kodi ndiwe ndani? Anthu afuna kudziŵa.’ Yohane anati: ‘Ndine mawu ofuula m’cipululu, ndipo nitsogolela anthu kwa Yehova, monga mmene Yesaya analoselela.’

Anthu anakondwela nazo zimene Yohane anali kuwaphunzitsa. Ambili anali kuganiza kuti mwina Yohane ndiye Mesiya. Koma iye anawauza kuti: ‘Wina wamkulu kuposa ine akubwela. Ine sindiyenela olo pang’ono kumuvula nsapato. Nimabatiza na madzi, koma iye adzakubatizani na mzimu woyela.’

“Munthu ameneyu anabwela monga mboni, kudzacitila umboni za kuwala, kuti anthu osiyanasiyana akhulupilile kudzela mwa iye.”—Yohane 1:7