Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 74

Yesu Anakhala Mesiya

Yesu Anakhala Mesiya

Yohane ankalalikira kuti: ‘Wina wamkulu kuposa ine akubwera.’ Pamene Yesu anali ndi zaka 30 anapita kumtsinje wa Yorodano kumene Yohane ankabatiza anthu. Pa nthawiyi Yesu ankachokera ku Galileya. Iye ankafuna kuti Yohane amubatize koma Yohaneyo anati: ‘Ayi, ine si woyenera kubatiza inu. Inuyo ndiye woyenera kundibatiza ine.’ Yesu anamuuza kuti: ‘Yehova akufuna kuti undibatize.’ Choncho anapita mumtsinje wa Yorodano ndipo Yohane anabatiza Yesu pomuviika thupi lonse.

Yesu atavuuka m’madzimo anayamba kupemphera. Ndiyeno kumwamba kunatseguka ndipo mzimu wa Mulungu wooneka ngati nkhunda unatsika n’kudzamutera. Kenako Yehova analankhula ali kumwamba kuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwera nawe.”

Mzimu wa Mulungu utafika pa Yesu, Yesuyo anakhala Khristu kapena kuti Mesiya. Choncho anayamba kugwira ntchito imene Mulungu anamutuma.

Yesu atangobatizidwa anapita m’chipululu ndipo anakhalamo masiku 40. Atachoka m’chipululumo anapita kukaona Yohane. Yohane ataona Yesu akubwera poteropo anati: ‘Uyu ndi Mwanawankhosa wa Mulungu amene akuchotsa uchimo wa dziko.’ Apa Yohane ankafuna kuti anthu adziwe kuti Yesu ndi Mesiya. Koma kodi ukudziwa zimene zinachitika pamene Yesu anali kuchipululu? Tiona m’mutu wotsatira.

“Panamveka mawu ochokera kumwamba akuti: ‘Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwera nawe.’”​—Maliko 1:11