Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 76

Yesu Anayeretsa Kachisi

Yesu Anayeretsa Kachisi

M’chaka cha 30 C.E., Yesu anapita ku Yerusalemu pa nthawi ya chikondwerero cha Pasika. Anthu enanso ambiri anapita ku Yerusalemuko kukachita chikondwererochi. Pa nthawiyi, anthu ankapereka nsembe za nyama pakachisi. Ena ankabweretsa nyamazi, koma ena ankagula ku Yerusalemu komweko.

Yesu atalowa m’kachisi anapeza kuti anthu akugulitsa nyama mmenemo. Tangoganiza! Ankachita malonda m’nyumba ya Yehovayi! Ndiye kodi Yesu anatani? Nthawi yomweyo anatenga zingwe n’kupanga chokwapulira. Ndiyeno anayamba kuthamangitsa nkhosa ndi ng’ombe zimene zinali m’kachisimo. Anagubuduzanso matebulo a anthu amene ankachita malondawo komanso anakhuthulira pansi ndalama zawo. Iye anauza anthu amene ankagulitsa nkhunda kuti: ‘Chotsani izi muno! Nyumba ya Bambo anga musaisandutse malo ochitira bizinezi!’

Anthu anadabwa kwambiri ndi zimene Yesu anachitazi. Ophunzira ake anakumbukira ulosi wonena za Mesiya wakuti: ‘Ndidzakhala wodzipereka kwambiri panyumba ya Yehova.’

M’chaka 33 C.E., Yesu anayeretsanso kachisi pothamangitsa anthu amene ankachita malonda panyumba ya Yehovayi. Iye sanalole kuti munthu aliyense azinyoza nyumba ya Yehova.

“Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.”—Luka 16:13