Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 78

Yesu Analalikila Uthenga wa Ufumu

Yesu Analalikila Uthenga wa Ufumu

Yesu atabatizika, anayamba kulalikila kuti: ‘Ufumu wa Mulungu wayandikila.’ Ophunzila ake anam’londola kumene anali kuyenda m’madela a ku Galileya na ku Yudeya. Pamene anabwelela kwawo ku Nazareti, anapita ku sunagoge. Ataloŵa anatsegula mpukutu wa Yesaya, na kuŵelenga mokweza kuti: ‘Yehova wanipatsa mzimu woyela kuti nilalikile uthenga wabwino.’ Kutanthauza ciani? Kutanthauza kuti, ngakhale kuti anthu anali kufuna kuona Yesu akucita zozizwitsa, cacikulu cimene analandilila mzimu woyela, cinali kulalikila uthenga wabwino. Ndiyeno anauza anthuwo kuti: ‘Lelo, ulosi uwu wakwanilitsika.’

Atacoka ku sunagoge, Yesu anayenda ku Nyanja ya Galileya. Kumeneko anapeza asodzi anayi. Iye anawaitana kuti: ‘Nitsatileni, nidzakupangani asodzi a anthu.’ Maina awo anali Petulo, Andireya, Yakobo, na Yohane. Nthawi imeneyo anasiya nchito yawo yakupha nsomba na kutsatila Yesu. Iwo analalikila m’madela onse a ku Galileya za Ufumu wa Yehova. Analalikila m’masunagoge, m’misika, na m’misewu. Kulikonse kumene anapita cikhamu ca anthu cinawalondola. Ndipo kulikonse anthu anamva za Yesu, mpaka ku Siriya.

M’kupita kwa nthawi, Yesu anapatsako ena mwa otsatila ake mphamvu zocilitsa anthu na kucotsa ziŵanda. Ena anali kuyenda na Yesu pokalalikila m’mizinda na m’midzi. Azimayi okhulupilika monga Mariya Mmagadala, Jowana, Suzana, komanso ena, anasamalila Yesu na ophunzila ake.

Yesu atawaphunzitsa nchito ophunzila ake, anaŵatumiza kuti akalalikile. Iwo analalikila m’madela onse a mu Galileya. Anthu ambili anakhala ophunzila a Yesu, ndipo anabatizika. Ambili anali kufuna kukhala ophunzila, cakuti Yesu anawayelekezela na munda wofunika kukolola. Iye anati: ‘Pemphani Yehova kuti atumize anchito ambili kuti agwile nchito yokolola.’ Pambuyo pake, anasankha anthu 70 pa ophunzila ake, na kuŵatumiza aŵili-aŵili kuti akalalikile m’madela onse a Yudeya. Iwo anaphunzitsa anthu onse osiyana-siyana za Ufumu wa Mulungu. Pamene anabwelako, anali osangalala kuuza Yesu mmene anayendela. Mdyelekezi sanakwanitse kulepheletsa nchito yolalikila.

Yesu anathandiza ophunzila ake kuti akapitilize kugwila nchito yofunika imeneyi, ngakhale iye atabwelela kumwamba. Anawauza kuti: ‘Lalikilani uthenga wabwino pa dziko lonse lapansi. Phunzitsani anthu Mawu a Mulungu, ndipo abatizeni.’

“Ndiyenela kukalengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, cifukwa ndi zimene anandituma kudzacita.”—Luka 4:43