Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 79

Yesu Acita Zozizwitsa Zambili

Yesu Acita Zozizwitsa Zambili

Yesu anabwela pa dziko lapansi kudzalengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Pofuna kuonetsa zimene Yesu adzacita akadzakhala Mfumu, Yehova anam’patsa mzimu woyela kuti acite zozizwitsa. Iye anali kucilitsa matenda alionse. Kulikonse kumene Yesu anali kuyenda, anthu anali kubwela kwa iye kuti awacilitse, ndipo anali kuwacilitsa onse. Osaona anayamba kuona, ogontha anayamba kumvela, komanso olemala anayamba kuyenda. Ndiponso anthu ovutitsidwa na ziŵanda, anawacotsa ziŵanda. Olo kugwilako cabe covala cake, anthu anali kucila. Ngakhale pamene Yesu anafuna kukhala kwa yekha, anthu akabwela sanali kuwabweza.

Tsiku lina anthu anabweletsa munthu wakufa ziwalo kumene Yesu anali. Koma popeza m’nyumbayo munali anthu ambili, iwo anakangiwa kuloŵa. Conco anaboola pa mtenje na kuloŵetselapo munthu wakufa ziwalo uja. Ndipo Yesu anauza munthu uja kuti: ‘Nyamuka uyambe kuyenda.’ Pamene anayamba kuyenda, anthu anadabwa kwambili.

Pa nthawi ina, Yesu poloŵa m’mudzi wina, anthu 10 akhate anaimilila capatali. Iwo ataona Yesu anayamba kufuula kuti: ‘A Yesu, tithandizeni!’ M’masiku amenewo, anthu akhate sanali kuloledwa kukhala pafupi na anthu ena. Yesu anauza anthu aja kuti apite kukacisi kuti akaonekele kwa ansembe. Izi n’zimene akhate anafunikila kucita akacilitsidwa, malinga na Cilamulo ca Yehova. Ali m’njila kupita kukacisi, anthuwo anacila. Mmodzi wa iwo ataona kuti wacila, anabwelela kukayamikila Yesu na kutamanda Mulungu. Pa anthu onse 10 aja, mmodzi cabe ndiye anayamikila Yesu.

Mzimayi wina wodwala kwa zaka 12, anali kufunitsitsa kuti acilitsidwe. Yesu ali pa cigulu ca anthu, mzimayiyo anabwela ca kumbuyo kwa Yesu, na kugwila m’mbali mwa covala cake. Pamenepo anacila. Izi zitacitika, Yesu anafunsa kuti: “Ndani wagwila malaya anga?” Mzimayiyo anacita mantha kwambili, koma anabwela poonekela na kuuza Yesu zoona. Yesu anatonthoza mzimayiyo kuti: ‘Mwanawe, pita mu mtendele.’

Mtsogoleli wina wa m’sunagoge, dzina lake Yairo, anacondelela Yesu kuti: ‘Tiyeni ku nyumba kwanga! Mwana wanga wamkazi ni wodwala kwambili.’ Koma Yesu akali m’njila kupita ku nyumba kwa Yairo, mwana uja anamwalila. Pamene Yesu anafika, anapeza anthu ambili amene anabwela ku malilo. Yesu anauza anthuwo kuti: ‘Musalile, cifukwa mwana uyu wagona cabe.’ Ndiyeno anagwila dzanja la mwana uja na kumuuza kuti: ‘Mwanawe, uka!’ Kamtsikana kaja kanauka. Kenako Yesu anauza makolo ake kuti am’patse cakudya. Ganizila cabe mmene makolo ake anamvelela!

“Mulungu anamudzoza ndi mzimu woyela ndi mphamvu. Ndiponso kuti popeza Mulungu anali naye, anayendayenda m’dziko, n’kumacita zabwino ndi kucilitsa onse osautsidwa ndi Mdyelekezi.”—Machitidwe 10:38