Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 81

Ulaliki wa Paphiri

Ulaliki wa Paphiri

Yesu atasankha atumwi ake 12, anatsika m’phiri n’kupita pamalo amene panasonkhana anthu ambiri. Anthuwo anali ochokera ku Galileya, Yudeya, Turo, Sidoni, Siriya komanso kutsidya kwa mtsinje wa Yorodano. Anamubweretsera anthu odwala matenda osiyanasiyana komanso amene ankavutitsidwa ndi ziwanda. Yesu anawachiritsa onsewo. Kenako anakhala pansi n’kuyamba kulankhula. Anafotokoza zimene munthu angachite ngati akufuna kuti Mulungu akhale mnzake. Yesu anatinso tiyenera kuzindikira kuti timafunika kutsogoleredwa ndi Yehova ndipo tiyenera kuphunzira za iye kuti tizimukonda. Koma ananena kuti sitingakonde Mulungu ngati sitikonda anzathu. Komanso tiyenera kuchitira zabwino aliyense, ngakhale adani athu.

Yesu anati: ‘Kungokonda anzanu si kokwanira. Muyenera kukondanso adani anu komanso muzikhululuka kuchokera pansi pa mtima. Ngati wina wakulakwirani, muzipita kukakambirana naye n’kupepesana. Muzichitira anthu zimene mungafune kuti iwonso akuchitireni.’

Yesu anaperekanso malangizo abwino okhudza chuma. Iye anati: ‘Kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu n’kofunika kwambiri kuposa kukhala ndi ndalama zambiri. Munthu angathe kukuberani ndalama koma sangakubereni ubwenzi wanu ndi Yehova. Siyani kudandaula kuti: “Mawa tidzadya chiyani, tidzamwa chiyani nanga tidzavala chiyani?” Ganizirani za mbalame. Mulungu amaonetsetsa kuti nthawi zonse zili ndi chakudya. Kudandaula sikungapangitse kuti mukhale ndi moyo wautali. Musaiwale kuti Yehova amadziwa zimene mukufunikira.’

Anthuwo anali asanamvepo munthu akulankhula ngati mmene Yesu ankalankhulira. Atsogoleri a chipembedzo anali asanawaphunzitsepo zimenezi. N’chifukwa chiyani Yesu ankatha kuphunzitsa bwino chonchi? Chifukwa choti zonse zimene ankaphunzitsa zinkachokera kwa Yehova.

“Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine, chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa.”​—Mateyu 11:29