Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 81

Ulaliki wa pa Phili

Ulaliki wa pa Phili

Yesu atatsiliza kusankha atumwi ake 12, anatsika m’phili n’kupita kumene khamu la anthu linasonkhana. Anthuwo anacokela ku Galileya, Yudeya, Turo, Sidoni, Siriya, na kutsidya kwa mtsinje wa Yorodano. Anabweletsa anthu odwala, komanso amene anali kuvutitsidwa na ziŵanda. Yesu anawacilitsa onse. Ndiyeno anakhala pansi kumbali kwa phililo na kuyamba kuwaphunzitsa. Anafotokoza zimene tiyenela kucita kuti tikhale mabwenzi a Mulungu. Tifunikila Yehova kuti azititsogolela, ndipo tiyenela kumukonda. Koma sitingakonde Mulungu ngati sitikonda anthu anzathu. Tiyenela kukhala acifundo komanso acilungamo kwa anthu onse, ngakhale amene amatizonda.

Yesu anati: ‘Musamakonde mabwenzi anu cabe. Muzikondanso adani anu, ndiponso kukhululukila ena na mtima wonse. Ngati mwakhumudwitsa wina, mwamsanga pitani mukam’pepese. Citilani ena zimene mungafune kuti akucitileni.’

Yesu anathandizanso anthuwo kupewa maganizo okonda cuma. Iye anati: ‘Ubwenzi na Yehova ni wofunika kuposa ndalama zambili. Kawalala angakubeleni ndalama, koma palibe munthu angakubeleni ubwenzi wanu na Yehova. Lekani kuda nkhawa kuti mudzadya ciani, mudzamwa ciani, kapena mudzavala ciani. Yang’anani mbalame. Mulungu amazipatsa cakudya cokwanila nthawi zonse. Nkhawa sizingawonjezele moyo wanu ngakhale na tsiku limodzi. Kumbukilani kuti Yehova amadziŵa zimene mufunikila.’

Anthuwo sanamvelepo munthu aliyense akuphunzitsa mmene Yesu anaŵaphunzitsila. Atsogoleli awo acipembedzo sanawaphunzitsepo zinthu zimenezo. N’cifukwa ciani Yesu anali mphunzitsi wabwino kwambili? Cifukwa zonse zimene anaphunzitsa zinacokela kwa Yehova.

“Senzani goli langa ndipo phunzilani kwa ine, cifukwa ndine wofatsa ndi wodzicepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa”—Mateyu 11:29