Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 85

Yesu Acilitsa pa Sabata

Yesu Acilitsa pa Sabata

Afarisi anali kumuzonda Yesu, ndipo anali kufuna kum’peza cifukwa kuti am’mange. Anali kukamba kuti Yesu sayenela kucilitsa odwala pa Sabata. Tsiku lina pa Sabata, Yesu anapeza munthu amene anali wosaona cibadwile, akupempha-pempha mu msewu. Ndiyeno anauza ophunzila ake kuti: ‘Onani mmene mphamvu ya Mulungu ithandizile munthu uyu.’ Pamenepo anasakaniza mata ake na dothi, n’kupanga matika. Basi anatenga matikawo n’kupaka munthuyo m’maso, n’kumuuza kuti: ‘Pita ukasambe m’maso pa dziŵe la Siloamu.’ Munthu uja anacita zimenezo, ndipo anayamba kuona. Mu umoyo wake wonse, aka kanali koyamba kuona.

Anthu anadabwa kwambili. Iwo anati: ‘Kodi munthu uyu si uja anali kukhala pansi n’kupempha-pempha, kapena ni wina angofanana cabe?’ Munthu uja anati: ‘Ndine amene, uja anabadwa wosaona!’ Conco anthu anamufunsa kuti: ‘Nanga zakhala bwanji kuti uyambe kuona?’ Atawafotokozela zimene zinacitika, anapita naye kwa Afarisi.

Munthu uja anauza Afarisiwo kuti: ‘Yesu ndiye wanipaka matika m’maso, na kuniuza kuti nikasambemo. N’tacita zimenezo, basi nayamba kuona.’ Afarisiwo anati: ‘Ngati Yesu amacilitsa pa Sabata, ndiye kuti mphamvuzo si zocokela kwa Mulungu.’ Koma anthu ena anati: ‘Ngati mphamvu zake si zocokela kwa Mulungu, sakanakwanitsa kucilitsa ngakhale pang’ono.’

Afarisiwo anaitana makolo a munthuyo, na kuwafunsa kuti: ‘Zakhala bwanji kuti mwana wanu ayambe kuona?’ Makolowo anacita mantha, cifukwa Afarisi anali ataopseza kuti aliyense amene adzakhulupilila mwa Yesu, adzacotsedwa m’sunagoge. Conco iwo anati: ‘Sitidziŵa. M’funseni ayankhe yekha.’ Afarisiwo anam’panikiza munthuyo na mafunso, mpaka anawauza kuti: ‘Nakuuzani kale zonse. Mukungonifunsabe mafunso cifukwa ciani?’ Apa lomba Afarisi anakwiya, na kum’thamangitsa.

Yesu anam’londola munthu uja, na kum’funsa kuti: ‘Kodi uli na cikhulupililo mwa Mesiya?’ Munthuyo anayankha kuti: ‘Sembe nimudziŵa, n’kanakhulupilila mwa iye.’ Yesu anati: ‘Mesiyayo ndine amene.’ Kodi sikunali kukoma mtima kumeneko? Sanangom’cilitsa cabe, koma anam’thandizanso kukhulupilila mwa Mesiya.

“Mukulakwitsa cifukwa simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu.”—Mateyu 22:29