Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 88

Am’gwila Yesu

Am’gwila Yesu

Yesu na ophunzila ake anadutsa m’Cigwa ca Kidironi popita ku Phili la Maolivi. Panali pakati pa usiku, ndipo mwezi kumwamba unali wathunthu. Atafika m’munda wa Getsemane, Yesu anauza atumwi ake kuti: “Khalani pansi pompano, ine ndikupita uko kukapemphela.” Basi Yesu anapita capatali na kugwada pansi. Movutika mtima kwambili, anapemphela kwa Yehova kuti: “Cifunilo canu cicitike.” Pamenepo Yehova anatuma mngelo kudzalimbikitsa Yesu. Atabwelela kwa atumwi ake, anapeza kuti iwo akugona. Yesu anati: ‘Ukani! Si nthawi yogona ino! Nthawi yakwana yakuti nipelekedwe m’manja mwa adani anga.’

Posapita nthawi, Yudasi anatulukila, ali na gulu la anthu atanyamula malupanga na zibonga. Yudasi ndiye anali patsogolo. Iye anali kudziŵa kumene angapeze Yesu, cifukwa kangapo konse anabwelapo naye pamodzi na atumwi ena ku munda wa Getsemane. Yudasi anauza asilikali kuti adzaŵapatsa cizindikilo, cakuti akam’dziŵe Yesu. Conco, iye anapita kwa Yesu na kumuuza kuti: ‘Muli bwanji Mphunzitsi,’ kenako anam’psompsona. Ndiyeno Yesu anati: ‘Yudasi, kodi ukunipeleka mwa kunipsompsona?’

Kenako Yesu anayandikila gulu lija, na kuwafunsa kuti: “Mufuna ndani?” Iwo anayankha kuti: “Yesu Mnazareti.” Yesu anati: “Ndine.” Atamva yankho lake, iwo anabwelela kumbuyo n’kugwa pansi. Yesu anaŵafusanso kuti: “Mufuna ndani?” Anayankhanso kuti: “Yesu Mnazareti.” Ndiyeno Yesu anaŵauza kuti: ‘Nakuuzani kale kuti ndine. Anawa alekeni apite.’

Petulo ataona zimenezo anasolola lupanga lake na kudula khutu la Makasi, kapolo wa mkulu wa ansembe. Koma Yesu anatenga khutu lija na kulibweza pamalo ake, ndipo anamucilitsa. Ndiyeno anauza Petulo kuti: ‘Bweza lupanga lako m’cimake. Ukapha munthu na lupanga, iwenso udzaphedwa na lupanga.’ Basi asilikaliwo anam’gwila Yesu na kum’manga manja, koma atumwi onse anathaŵa. Gulu lija linapita naye kwa Anasi wansembe wamkulu. Anasi anafunsa Yesu mafunso ambili-mbili. Pambuyo pake anam’tumiza kwa Kayafa Mkulu wa Ansembe. Nanga n’ciani cinacitika kwa atumwi?

“M’dzikomu mukumana ndi masautso, koma limbani mtima. Ndaligonjetsa dziko ine.”—Yohane 16:33