Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 89

Petulo Akana Yesu

Petulo Akana Yesu

Pamene Yesu anali na atumwi ake m’cipinda capamwamba, anaŵauza kuti: ‘Usiku uno, nonsenu mudzathaŵa na kunisiya nekha.’ Koma Petulo anati: ‘Koma osati ine! Ngakhale aŵa onse akusiyeni, ine sinidzakusiyani.’ Yesu anauza Petulo kuti: ‘Tambala akalibe kulila, iwe udzanikana katatu kuti sunidziŵa.’

Pamene asilikali anatengela Yesu ku nyumba ya Kayafa, atumwi ambili anathaŵa. Koma aŵili analondola m’cigulu ca anthu. Mmodzi wa iwo anali Petulo. Iye analoŵa mpaka m’bwalo la nyumba ya Kayafa, na kuyamba kuwotha moto. Moto utawala, mtsikana wanchito anam’zindikila Petulo, ndipo anati: ‘Nakudziŵani! Munali pamodzi na Yesu!’

Petulo anati: ‘Iyai, sindine! Nkhani imene ukamba siniidziŵa ine!’ Basi ananyamuka kuti akatuluke pa geti. Koma mtsikana winanso wanchito anamuona, ndipo anauza gulu la anthu kuti: ‘Nayenso uyu anali na Yesu!’ Koma Petulo anati: ‘Yesu uyo ine sinim’dziŵa olo pang’ono!’ Ndiyeno mwamuna wina anati: ‘Ndiwe mmodzi wa iwo! Ngakhale kakambidwe kako n’ka ku Galileya, kumene Yesu acokela.’ Koma Petulo anacita kulumbila, amvekele: ‘Ine munthu ameneyo sinim’dziŵa!’

Pa nthawi imeneyo tambala analila. Kenako Petulo anaona Yesu akuceuka kumuyang’ana. Anakumbukila mawu a Yesu, ndipo anacoka panja na kuyamba kulila kwambili.

Oweluza a Khoti Yaikulu ya Ayuda, anasonkhana ku nyumba kwa Kayafa kuti aweluze mlandu wa Yesu. Iwo anali atagwilizana kale zakuti aphe Yesu. Apa anali kungofuna kum’peza cifukwa. Koma sanam’peze na mlandu uliwonse. Kayafa anangom’funsa mwacindunji kuti: ‘Kodi ndiwe Mwana wa Mulungu?’ Yesu anayankha kuti: ‘Inde.’ Kayafa anati: ‘Basi, sipafunikilanso umboni wina. Munthu uyu akunyoza Mulungu!’ Iwo anagwilizana kuti: ‘Munthu uyu afunika kuphedwa.’ Ena anayamba kum’menya mambama, kum’thila mata, kum’phimba kumaso, kum’menya kenako n’kumuuza kuti: ‘Ngati ndiwe mneneli, tiuze wakumenya n’ndani?’

Kutaca, anatenga Yesu kupita naye ku Khoti Yaikulu ya Ayuda. Kumeneko anam’funsanso kuti: ‘Kodi ndiwe Mwana wa Mulungu?’ Yesu poyankha anati: ‘Mwakamba mwekha kuti ndine Mwana wa Mulungu.’ Basi pamenepo anam’patsa mlandu wakuti wanyoza Mulungu. Anapita naye kwa bwanamkubwa waciroma, Pontiyo Pilato. Ndiyeno cinacitika n’ciani? Tidzaona m’nkhani yokonkhapo.

“Nthawi . . . yafika kale. Mubalalika aliyense kupita kunyumba kwake, ndipo mundisiya ndekha. Koma sindikhala ndekha, cifukwa Atate ali ndi ine.”—Yohane 16:32