Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 90

Yesu Aphedwa ku Gologota

Yesu Aphedwa ku Gologota

Ansembe aakulu anatenga Yesu kupita naye ku nyumba kwa bwanamkubwa Pilato. Pilato anafunsa anthuwo kuti: ‘Kodi munthu uyu mwam’peza na mlandu wanji?’ Iwo anati: ‘Iye akuti ni mfumu!’ Pilato anafunsa Yesu kuti: “Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.”

Kenako Pilato anatumiza Yesu kwa Herode, wolamulila wa ku Galileya. Anacita izi kuti aone ngati angam’peze na mlandu uliwonse. Koma nayenso Herode sanam’peze na mlandu uliwonse, ndipo anam’bwezanso kwa Pilato. Ndiyeno Pilato anauza anthuwo kuti: ‘Ine na Herode sitinam’peze na mlandu uliwonse munthu uyu. Conco nim’masula.’ Koma anthuwo anayamba kufuula, amvekele: ‘Aphedwe! Aphedwe!’ Basi asilikali anayamba kum’kwapula Yesu, kum’thila mata, na kum’menya. Anamuvalika cisoti caminga, n’kumutonza, amvekele: ‘Tikuoneni Mfumu ya Ayuda.’ Pilato anauzanso anthuwo kuti: ‘Sin’namupeze na mlandu uliwonse munthu uyu.’ Koma iwo anafuulabe kuti: “Apacikidwe ameneyo!” Conco, Pilato anapeleka Yesu kuti akam’pacike.

Asilikaliwo anatenga Yesu n’kupita naye ku malo ochedwa Gologota. Kumeneko anam’khomelela pa mtengo na kuuimilika. Yesu anapemphela kuti: ‘Atate, akhululukileni, sadziŵa zimene akucita.’ Anthuwo anayamba kum’seka Yesu, amvekele: ‘Ngati ndiwedi Mwana wa Mulungu, seluka pa mtengo apo! Dzipulumutse tione.’

Munthu wacifwamba amene anam’pacika pambali pake anati: “Mukandikumbukile mukakaloŵa mu Ufumu wanu.” Yesu analonjeza munthuyo kuti: ‘Udzakhala na ine m’Paradaiso.’ Ndiyeno kumasana, kunacitika mdima m’dzikomo kwa maola atatu. Ena mwa ophunzila ake anali ciimilile pa mtengo umene anam’pacikapo, kuphatikizapo Mariya, mayi wake wa Yesu. Ndipo Yesu anauza Yohane kuti azisamalila Mariya, pomutenga ngati mayi wake wom’bala.

Pothela pake, Yesu anati: “Ndakwanilitsa cifunilo canu!” Anaŵelamila pansi n’kumwalila. Pamenepo kunacitika civomezi camphamvu. Mu kacisi, cinsalu colekanitsa Cipinda Coyela na Cipinda Coyela Koposa cinang’ambika pakati. Ndipo msilikali anati: ‘Uyu analidi Mwana wa Mulungu.’

“Malonjezo a Mulungu, kaya akhale oculuka cotani, akhala inde kudzela mwa iye.”—2 Akorinto 1:20