Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 91

Yesu Aukitsidwa

Yesu Aukitsidwa

Yesu atamwalila, munthu wina wolemela dzina lake Yosefe, anapempha kwa Pilato kuti acotse thupi la Yesu pa mtengo. Atamulola, Yosefe anakulunga thupi la Yesu m’nsalu zabwino na kum’paka mafuta onunkhila. Kenako anamuika m’manda atsopano. Pakhomo pake anavalapo na cimwala colema. Ansembe aakulu anauza Pilato kuti: ‘Tili na nkhawa kuti mwina ophunzila a Yesu angabe thupi lake na kuyamba kunamiza anthu kuti wauka.’ Conco Pilato anaŵauza kuti: ‘Mutsekepo zolimba pa mandapo, ndipo muikepo alonda.’

Patapita masiku atatu, azimayi ena anacelela m’mamawa kupita ku manda. Atafika, anapeza kuti cimwala cija acicotsapo. Poyang’ana mkati mwa manda, anaonamo mngelo, ndipo anaŵauza kuti: ‘Musacite mantha. Yesu waukitsidwa. Pitani mukauze ophunzila ake kuti akakumane naye ku Galileya.’

Mariya Mmagadala anafulumila kukauza Petulo na Yohane. Anaŵauza kuti: ‘Pali amene watenga thupi la Yesu!’ Petulo na Yohane anathamangila ku manda kuja. Atapeza kuti m’manda mulibedi kanthu, anangobwelela ku manyumba kwawo.

Mariya atabwelelanso kumanda kuja, anaona angelo aŵili mkati mwa mandawo. Iye anauza angelowo kuti: ‘Sinidziŵa kumene aŵapeleka Ambuye.’ Kenako anaona mwamuna wina wake. Poganiza kuti munthuyo ni wosamalila munda, Mariya anati: ‘Bambo, conde niuzeni kumene mwapeleka Yesu.’ Munthuyo atachula kuti, “Mariya!” iye anazindikila kuti ni Yesu. Pamenepo Mariya anafuula kuti: “Mphunzitsi!” na kum’kumbatila. Yesu anauza Mariya kuti: ‘Pita ukauze abale anga kuti waniona.’ Basi Mariya anathamanga kupita kwa ophunzila, kukaŵauza kuti waona Yesu.

Pa nthawi ina yake tsikulo, ophunzila aŵili anali kuyenda, kucokela ku Yerusalemu kupita ku Emau. Munthu anangoonekela n’kumayenda nawo pamodzi. Munthuyo anawafunsa zimene anali kukambilana. Ophunzilawo anati: ‘Kodi simunamve? Masiku atatu apitawa, ansembe aakulu anapha Yesu. Koma azimayi ena akuti iye ali moyo!’ Munthuyo anafunsa kuti: ‘Kodi mumakhulupilila mawu a aneneli? Paja anati Khristu adzaphedwa, kenako adzaukitsidwa.’ Munthuyo anapitiliza kuwafotokozela Malemba. Atafika ku Emau, ophunzilawo anapempha munthuyo kuti apite nawo. Pa cakudya camadzulo, munthuyo atapemphelela cakudyaco, ophunzilawo anazindikila kuti ni Yesu. Kenako iye anasoŵa.

Ophunzila aŵiliwo anathamangila ku Yerusalemu, ku nyumba imene atumwi ena anasonkhanako. Ndipo anawasimbila zimene zinacitika. Ali m’nyumbamo, Yesu anaonekela kwa onse. Poyamba atumwiwo sanakhulupilile kuti anali Yesu. Ndiyeno Yesu anaŵauza kuti: ‘Onani manja anga, nigwileni. Zinaloseledwa kuti Khristu adzaukitsidwa kwa akufa.’

“Ine ndine njila, coonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzela mwa ine.”—Yohane 14:6