Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 93

Yesu Abwelela Kumwamba

Yesu Abwelela Kumwamba

Yesu atakumana na ophunzila ake ku Galileya, anawapatsa lamulo lofunika kwambili lakuti: ‘Pitani, kapangeni ophunzila m’maiko onse. Mukawaphunzitse zimene ine n’nakuphunzitsani, ndipo mukaŵabatize.’ Ndiyeno anawalonjeza kuti: ‘Kumbukilani kuti n’dzakhala na imwe nthawi zonse.’

Yesu anakhala masiku 40 pambuyo poukitsidwa. Pa nthawiyi anaonekela kwa ophunzila ake ambili ku Galileya na ku Yerusalemu. Ndipo anawaphunzitsa zinthu zambili zofunika, komanso anacita zozizwitsa zoculuka. Kenako, Yesu anakumana na atumwi ake komaliza pa Phili la Maolivi. Ali ku Yerusalemu, Yesu anauza atumwi ake kuti: ‘Musacoke mu Yerusalemu. Yembekezelanibe zimene Atate analonjeza.’

Atumwi ake sanamvetsetse zimene Yesu anatanthauza. Conco anam’funsa kuti: ‘Kodi tsopano mudzakhala Mfumu ya Isiraeli?’ Yesu anayankha kuti: ‘Iyai, nthawi ya Yehova yakuti nikhale Mfumu sinakwane. Posacedwa mudzalandila mphamvu ya mzimu woyela, ndipo mudzakhala mboni zanga. Pitani mukalalikile ku Yerusalemu, ku Yudeya, ku Samariya, mpaka ku malekezelo a dziko lapansi.’

Pamenepo Yesu ananyamuka n’kuyamba kukwela kumwamba, mpaka anaphimbika m’mitambo. Ophunzila ake anali kungoyang’ana kumwamba, koma sanaonekenso.

Ophunzila ake anaseluka m’Phili la Maolivi n’kupita ku Yerusalemu. Anali kukumana kaŵili-kaŵili m’cipinda capamwamba na kupemphela. Anali kuyembekezela kuti Yesu aŵapatse malangizo owonjezeleka.

“Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika”—Mateyu 24:14