Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 94

Ophunzira a Yesu Analandira Mzimu Woyera

Ophunzira a Yesu Analandira Mzimu Woyera

Patatha masiku 10 kuchokera pamene Yesu anapita kumwamba, ophunzira ake analandira mzimu woyera. Linali tsiku la mwambo wa Pentekosite m’chaka cha 33 C.E. Mu Yerusalemu munali anthu ambiri ochokera m’madera osiyanasiyana amene anabwera kumwambowu. Ophunzira a Yesu okwana 120 anasonkhana m’chipinda china chapamwamba. Mwadzidzidzi, panachitika zinthu zodabwitsa. Tinthu tina tooneka ngati malawi a moto tinaoneka pamutu pa wophunzira aliyense ndipo onsewo anayamba kulankhula m’zilankhulo zosiyanasiyana. Kenako mkokomo wangati mphepo yamphamvu unamveka panyumba yonseyo.

Anthu amene anabwera ku Yerusalemu aja anamva mkokomowu ndipo anathamangira kunyumba yomwe kunali ophunzirawo kuti akaone chimene chikuchitika. Anadabwa kwambiri atamva kuti ophunzirawo akulankhula m’zilankhulo zosiyanasiyana. Anthuwo anati: ‘Komatu anthuwa ndi a ku Galileya. Ndiyeno zikutheka bwanji kuti azilankhula zilankhulo zathu?’

Kenako Petulo ndi atumwi ena anaimirira n’kuyamba kulankhula ndi anthuwo. Petulo anawafotokozera kuti Yesu anaphedwa ndipo Yehova anamuukitsa. Ndiyeno anati: ‘Panopa Yesu ali kumwamba kudzanja lamanja la Mulungu ndipo watipatsa mzimu woyera umene anatilonjeza. N’chifukwa chake mukuona zodabwitsazi.’

Anthuwo anakhudzidwa mtima kwambiri ndi zimene Petulo ananena moti anafunsa kuti: “Tichite chiyani pamenepa?” Iye anawauza kuti: ‘Lapani machimo anu ndipo mubatizidwe m’dzina la Yesu. Mukatero nanunso mulandira mzimu woyera.’ Pa tsikuli anthu pafupifupi 3,000 anabatizidwa. Zitatero, ophunzira anayamba kuwonjezeka kwambiri mu Yerusalemu. Mzimu woyera unkathandiza kwambiri atumwi ndipo anakhazikitsa mipingo kuti azitha kuphunzitsa anthu zinthu zonse zimene Yesu anawalamula.

“Ngati ukulengeza kwa anthu ‘mawu amene ali m’kamwa mwakowo,’ akuti Yesu ndiye Ambuye, ndipo mumtima mwako ukukhulupirira kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.”​—Aroma 10:9