Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 94

Ophunzila a Yesu Alandila Mzimu Woyela

Ophunzila a Yesu Alandila Mzimu Woyela

Patapita masiku 10 Yesu atabwelela kumwamba, ophunzila ake analandila mzimu woyela. Panali pa Pentekosite wa mu 33 C.E., ndipo anthu ocokela ku madela olekana-lekana anabwela ku Yerusalemu ku cikondwelelo ca Pentekosite. Ophunzila a Yesu analipo pafupi-fupi 120 m’cipinda capamwamba m’nyumba ina yake. Mwadzidzidzi panacitika zodabwitsa. Tunthu tooneka monga malawi a moto tunaonekela pamitu ya ophunzila onse, ndipo onse anayamba kukamba vitundu vosiyana-siyana. Kenako m’nyumbamo munamveka mkokomo monga wa cimphepo ca mkuntho.

Alendo ocokela ku madela ena, amene anabwela ku Yerusalemu anamva mkokomo umenewo, ndipo anathamangila ku nyumbayo kuti akaone zimene zinali kucitika. Anadabwa kuona kuti ophunzilawo akukamba vitundu va alendowo. Ndipo alendowo anati: ‘Anthu awa ni a ku Galileya. Nanga zitheka bwanji kuti azikamba vitundu vathu?’

Pamenepo Petulo na atumwi ena anaimilila kutsogolo kwa anthuwo. Ndiyeno anayamba kuŵauza mmene anthu anaphela Yesu, komanso kuti Yehova anamuukitsa kwa akufa. Petulo anati: ‘Tsopano Yesu ali kumwamba kudzanja lamanja la Mulungu, ndipo iye wapeleka mzimu woyela umene analonjeza. Ndiye cifukwa cake mwaona komanso kumva zozizwitsa izi.’

Anthuwo anakhudzika kwambili na mawu a Petulo, cakuti anam’funsa kuti: “Kodi tiyenela kucita ciani?” Iye anaŵauza kuti: ‘Lapani macimo anu ndipo mubatizike m’dzina la Yesu. Inunso mudzalandila mphatso ya mzimu woyela.’ Pa tsikulo, anthu pafupi-fupi 3,000 anabatizika. Kucokela pa nthawiyo, ophunzila anayamba kuwonjezeleka mofulumila kwambili mu Yerusalemu. Mothandizidwa na mzimu woyela, atumwiwo anapanga mipingo yambili kuti aziphunzitsa zinthu zonse zimene Yesu anawalamula.

“Ngati ukulengeza kwa anthu ‘mawu amene ali m’kamwa mwakowo,’ akuti Yesu ndiye Ambuye, ndipo mumtima mwako ukukhulupilila kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.” —Aroma 10:9