Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 95

Palibe Akanawaletsa Kulalikila

Palibe Akanawaletsa Kulalikila

Panali munthu wina wosakwanitsa kuyenda, nthawi zonse anali kukhala pa geti ya kacisi akupempha-pempha. Tsiku lina masana, anaona Petulo na Yohane akuloŵa m’kacisi. Ndiyeno anati kwa iwo: ‘Nipatsenkoni kangacepe.’ Petulo anati: ‘Nikupatsa cinthu cofunika kuposa ndalama. M’dzina la Yesu, nyamuka uyende!’ Basi Petulo anathandiza munthuyo kuimilila, ndipo anayamba kuyenda! Anthu anakondwela kwambili na cozizwitsaci, ndipo ambili anakhala okhulupilila.

Koma ansembe na Asaduki anakalipa kwambili. Anagwila atumwiwo na kuŵapeleka ku khoti. Kumeneko anawafunsa kuti: ‘Ndani wakupatsani mphamvu kuti mucilitse munthu uyu?’ Petulo anayankha kuti: ‘Yesu Khristu amene imwe munamupha, ndiye anatipatsa mphamvu.’ Atsogoleli acipembedzowo anakalipa, amvekele: ‘Mulekeletu kukamba za Yesu!’ Koma atumwi anati: ‘Tifunika kukamba za iye, sitingaleke.’

Atangowamasula aŵiliwo, anapita kukauza ophunzila ena zimene zinacitika. Iwo anapemphela capamodzi, ndipo anapempha Yehova kuti: ‘Conde tithandizeni kukhala olimba mtima kuti tipitilize kugwila nchito yanu.’ Yehova anawapatsa mzimu wake woyela, ndipo anapitiliza kulalikila na kucilitsa anthu. Anthu ambili anakhala okhulupilila. Koma Asaduki anaipidwa nazo kwambili, cakuti anagwila atumwi na kuwaponya mu jele. Koma usiku, Yehova anatumiza mngelo, ndipo anatsegula zitseko za jeleyo na kuuza atumwiwo kuti: ‘Bwelelani ku kacisi, mukaphunzitse kumeneko.’

Kutangoca m’mawa mwake, Khoti Yaikulu ya Ayuda ya atsogoleli acipembedzo inauzidwa kuti: ‘Zitseko za ndende n’zokhoma, koma amuna aja amene munawagwila mulibe! Iwo ali m’kacisi ndipo akuphunzitsa anthu!’ Basi anawagwilanso atumwiwo n’kuŵapeleka ku Khoti Yaikulu ya Ayuda. Mkulu wa ansembe anati: ‘Kodi sitinakulamuleni kuti mulekeletu kukamba za Yesu?’ Petulo anayankha kuti: “Ife tiyenela kumvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.”

Atsogoleli acipembedzowo anakwiya kwambili cakuti anali kufuna kupha atumwiwo. Koma Mfarisi wina, Gamaliyeli, anaimilila na kukamba kuti: ‘Samalani! Mwina Mulungu ali ndi anthu awa. Kodi mufuna kulimbana na Mulungu?’ Iwo anamvela mawu ake. Conco, iwo anangokwapula atumwiwo na kuwalamulanso kuti aleke kulalikila. Kenako anaŵaleka kuti apite. Koma atumwi sanaleke kulalikila. Anapitiliza kulalikila uthenga wabwino molimba mtima. Inde, analalikila m’kacisi, komanso ku nyumba na nyumba.

“Ife tiyenela kumvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.” —Machitidwe 5:29