Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 98

Cikhristu Cifalikila Kumadela Akutali

Cikhristu Cifalikila Kumadela Akutali

Atumwi anamvela lamulo la Yesu lakuti alalikile uthenga wabwino pa dziko lonse lapansi. Mu 47 C.E., abale a ku Antiokeya anatumiza Paulo na Sila pa ulendo wokalalikila. Alaliki acangu aŵiliwa anafika ku madela ambili a ku Asia Minor, monga ku Debe, Lusitara, komanso Ikoniyo.

Paulo na Baranaba anali kulalikila anthu osiyana-siyana, olemela komanso osauka, acicepele komanso acikulile. Ndipo anthu ambili analandila coonadi conena za Khristu. Paulo na Baranaba ali mkati molalikila bwanamkubwa wina wa ku Kupuro, dzina lake Serigio Paulo, panabwela munthu wina wamatsenga amene anayesa kuŵaletsa kulalikila. Paulo anauza munthuyo kuti: ‘Yehova akulange.’ Nthawi yomweyo wamatsenga uja analeka kuona. Serigio Paulo poona zimenezi, anakhala wokhulupilila.

Paulo na Baranaba analalikila kulikonse, ku nyumba na nyumba, m’mamaketi, m’misewu, komanso m’masunagoge. Pamene iwo anacilitsa munthu wina wolemala ku Lusitara, anthu amene anaona cozizwitsaco anaganiza kuti Paulo na Baranaba anali milungu, ndipo anafuna kuyamba kuŵalambila. Koma iwo anaŵaletsa na kuŵauza kuti: ‘Mufunika kulambila Mulungu yekha! Na ife ndife anthu monga imwe.’ Koma panabwela Ayuda ena amene anapangitsa anthuwo kuukila Paulo. Anam’ponya miyala Paulo na kumuguguzila kunja kwa mzinda. Anam’siya atakomoka poganiza kuti wafa. Koma Paulo anali akali moyo! Mwamsanga, abale anabwela kudzam’thandiza; anam’tenga na kuloŵa naye mu mzinda. Patapita nthawi, Paulo anabwelela ku Antiokeya.

Mu 49 C.E., Paulo anapitanso pa ulendo wina. Ataonanso abale ku Asia Minor, anapitiliza kukafalitsa uthenga wabwino mpaka kumadela a ku Ulaya. Anafika ku Atene, Aefeso, Filipi, Tesalonika, mpaka ku madela ena akutali. Sila, Luka, na mnyamata wina dzina lake Timoteyo, anayenda pamodzi na Paulo. Pogwilila nchito pamodzi anakhazikitsa mipingo na kuilimbitsa. Paulo anakhala mu Korinto kwa caka cimodzi na hafu, kuti alimbikitse abale a kumeneko. Anali kulalikila, kuphunzitsa, na kulembela makalata mipingo. Anali kugwilanso nchito yopanga matenti. M’kupita kwa masiku, anabwelelanso ku Antiokeya.

Mu 52 C.E., Paulo anapitanso pa ulendo wina wacitatu. Ulendowo anauyambila ku Asia Minor. Analoŵela ca kumpoto kukafika ku Filipi mpaka ku Korinto. Anakhala zaka zingapo ku Aefeso. Kumeneko, iye anali kuphunzitsa, kucilitsa, na kuthandiza mpingo. Analinso kukamba nkhani za anthu onse tsiku lililonse m’holo ya pa sukulu. Anthu ambili anamvetsela na kusintha makhalidwe awo. Pambuyo polalikila uthenga wabwino ku madela ambili, Paulo anapita ku Yerusalemu.

“Conco pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse.”—Mateyu 28:19