Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 103

“Ufumu Wanu Ubwele”

“Ufumu Wanu Ubwele”

Yehova analonjeza kuti: ‘Sipadzakhalanso kulila, zopweteka, kudwala, kapena imfa. Nidzapukuta misozi yonse m’maso mwawo. Zoipa zonse sizidzakumbukikanso.’

Yehova anaika Adamu na Hava m’munda wa Edeni, kuti akhale na umoyo wacimwemwe komanso mwamtendele. Anafunika kulambila Atate wawo wakumwamba, na kubala ana mpaka kudzaza dziko lapansi. Adamu na Hava sanamvele Yehova, koma zimenezi sizinasinthe colinga cake. M’buku lino, taona kuti zonse zimene Mulungu amalonjeza zimacitika. Ufumu wake udzabweletsa madalitso osaneneka pa dziko lapansi, monga mmene analonjezela kwa Abulahamu.

Posacedwa, Satana na ziŵanda zake, pamodzi na anthu onse oipa adzawonongedwa. Anthu onse pa dziko adzayamba kulambila Yehova. Sitidzadwalanso kapena kufa. M’malo mwake, tsiku lililonse tidzayamba kuuka tili na mphamvu, komanso okondwela kuti tili na moyo. Dziko lapansi lidzakhala paradaiso. Aliyense adzakhala na zakudya zabwino na nyumba zabwino. Anthu adzakhala okoma mtima, osati ankhanza kapena aciwawa. Nyama zamsanga sizidzayopa anthu, na ise sitidzaziyopa.

Idzakhala nthawi yokondweletsa kwambili pamene Yehova adzayamba kuukitsa anthu amene anafa. Tidzalandilanso anthu akale monga Abele, Nowa, Abulahamu, Sara, Mose, Rute, Esitere, na Davide. Nawonso adzagwilako nchito yokonza dziko lapansi kukhala paradaiso. Ndipo padzakhala nchito zambili zokondweletsa.

Yehova afuna kuti mukakhaleko pa nthawi imeneyo. M’pamene mudzafika pom’dziŵa bwino kwambili Yehova. Tiyeni tipitilize kulimbitsa ubwenzi wathu na Yehova tsiku na tsiku, lelo mpaka muyaya wonse!

“Ndinu woyenela, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandila ulemelelo ndi ulemu, cifukwa munalenga zinthu zonse.”—Chivumbulutso 4:11