Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kalata Yocokela ku Bungwe Lolamulila

Kalata Yocokela ku Bungwe Lolamulila

Okondedwa Abale na Alongo:

Monga alambili a Yehova, timakonda Mawu ake, Baibo. Ndife otsimikiza kuti Baibo imafotokoza mbili yakale molondola, imapeleka citsogozo codalilika kuti tikhale na umoyo wabwino, komanso timapezamo umboni wolimbikitsa wakuti Yehova amakondadi anthu. (Salimo 119:105; Luka 1:3; 1 Yohane 4:19) Mocokela pansi pa mtima, timafunitsitsa kuthandiza ena kuti adziŵe coonadi copezeka m’Mawu a Mulungu. Pa cifukwa cimeneci, ife a Bungwe Lolamulila, ndife okondwa kutulutsa buku ino yakuti, “Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo.” Lekani tikuunikileni pang’ono za buku ino.

Kweni-kweni buku ino tinailembela ana. Komabe, ingagwilenso nchito pothandiza anthu akulu-akulu ofuna kudziŵa zambili za m’Baibo. Ndipo popeza Baibo ni buku la aliyense, sitikaikila kuti tonse tingapindule na maphunzilo amene tingatengemo kuti tipeze cimwemwe ceni-ceni.

Buku ino ifotokoza mbili ya m’Baibo ya zocitika za mtundu wa anthu kucokela paciyambi. Tinayesetsa kufotokoza nkhani za m’Baibo m’njila yosavuta kumva, komanso motsatila ndondomeko ya mmene zinthuzo zinacitikila.

Koma buku ino siimangosimba zocitika za m’Baibo basi. Mawu ake komanso mapikica ake, anakonzedwa mwa njila yopangitsa nkhani za m’Baibo kuoneka monga zikucitika lelo, na kucititsa woŵelenga kukhudzika na nkhanizo.

Buku ino idzatithandiza kuona kuti Baibo imatiuza za anthu eni-eni amene anamvela Yehova, komanso amene sanamumvele. Idzatithandizanso kuphunzilapo kanthu kwa anthuwo. (Aroma 15:4; 1 Akorinto 10:6) Buku ino ili na zigawo 14. Mawu oyamba a cigawo ciliconse aunika maphunzilo akulu-akulu amene tingatengemo m’cigawoco.

Ngati ndimwe kholo, mungamaŵelenge nkhani yonse na mwana wanu, kenako n’kukambilana mapikica ali mmenemo. Mukatha apo, mungaŵelenge Malemba amene pacokela nkhaniyo. Thandizani mwana wanu kuona kuti maphunzilo amene akutengapo m’nkhaniyo ni ocokela m’Baibo. N’cimodzi-modzinso pophunzila na munthu wamkulu. Aziona kuti zimene akuphunzilazo zikucokela m’Baibo.

Tikhulupilila kuti buku ino idzathandiza onse a maganizo abwino, acicepele ngakhale akulu-akulu. Inde, kuŵathandiza kuphunzila Mawu a Mulungu, na kuŵagwilitsila nchito mu umoyo wawo. Cotulukapo cake, nawonso angayambe kulambila Yehova monga a m’banja lake lokondedwa.

Ndife abale anu,

Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova