Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mawu Oyamba a Cigawo 3

Mawu Oyamba a Cigawo 3

Pambuyo pa Cigumula, Baibo imangochula anthu ocepa amene anatumikila Yehova. Mmodzi wa iwo ni Abulahamu, amene anadziŵika monga bwenzi la Yehova. Koma n’cifukwa ciani anachedwa bwenzi la Yehova? Ngati ndimwe kholo, thandizani mwana wanu kudziŵa kuti Yehova amam’konda, na kuti amafuna kum’thandiza. Monga mmene anacitila Abulahamu, komanso amuna ena okhulupilika, monga Loti na Yakobo, na ise tingapemphe thandizo kwa Yehova momasuka. Tingakhale na cidalilo cakuti Yehova adzacita zonse zimene walonjeza.

M'CIGAWO CINO

PHUNZILO 7

Nsanja ya Babele

Anthu anafuna kumanga mzinda na nsanja yaitali yokafika kumwamba kweni-kweni. N’cifukwa ciani Mulungu mwadzidzidzi anawacititsa kuyamba kukamba vitundu vosiyana-siyana?

PHUNZILO 8

Abulahamu na Sara Anamvela Mulungu

N’cifukwa ciani Abulahamu na Sara anasiya umoyo wabwino n’kupita ku dziko la Kanani kukakhala alendo?

PHUNZILO 9

Mpaka anakhala na mwana wake!

Kodi Mulungu anakwanilitsa bwanji lonjezo lake kwa Abulahamu? Ni mwana uti wa Abulahamu amene kupitila mwa iye, lonjezo limeneli linakwanilitsidwa—Isaki kapena Isimaeli?

PHUNZILO 10

Kumbukilani Mkazi wa Loti

Mulungu anagwetsa moto na sulufule pa Sodomu na Gomora. N’cifukwa ciani mizinda imeneyi inawonongedwa? N’cifukwa ciani tiyenela kukumbukila mkazi wa Loti?

PHUNZILO 11

Cikhulupililo Ciyesedwa

Mulungu anauza Abulahamu kuti: ‘Tenga mwana wako mmodzi yekhayo ndipo ukamupeleke nsembe pa phili ku Moriya.’ Kodi Abulahamu akanacita ciani na nkhani yoyesa cikhulupililo imeneyi?

PHUNZILO 12

Yakobo Analandila Coloŵa

Isaki na Rabeka pamodzi na ana awo aŵili amphundu. Maina awo anali Esau na Yakobo. Popeza Esau ndiye anali woyamba kubadwa, anali kudzalandila coloŵa capadela. N’cifukwa ciani anasinthanitsa coloŵaco na mbale imodzi ya cakudya?

PHUNZILO 13

Yakobo na Esau Akhalanso pa Mtendele

N’cifukwa ciani Yakobo anadalitsidwa na mngelo? Nanga anacita ciani kuti akhalenso pa mtendele na Esau?