Mawu Oyamba a Cigawo 4
Cigawo cino cifotokoza za Yosefe, Yobu, Mose, komanso Aisiraeli. Onsewa anavutika kwambili cifukwa ca Mdyelekezi. Ena anacitilidwa zopanda cilungamo, kuponyewa m’ndende, kuikidwa ukapolo, ngakhale kufedwa okondedwa awo mwadzidzidzi. Ngakhale n’telo, Yehova anawateteza m’njila zolekana-lekana. Ngati ndimwe kholo, thandizani mwana wanu kumvetsa mmene atumiki a Yehova anavutikila, koma osataya cikhulupililo cawo.
Yehova anaseŵenzetsa Milili 10 kuonetsa kuti iye ni wamphamvu ngako kupambana milungu yonse ya Aiguputo. Fotokozani mmene Yehova anatetezela anthu ake kumbuyoko, na mmene amawatetezela masiku ano.
M'CIGAWO CINO
PHUNZILO 14
Kapolo Amene Anamvela Mulungu
Yosefe anali kucita zabwino, koma anakumanabe na mavuto aakulu. Cifukwa ciani?
PHUNZILO 15
Yehova Sanamuiŵalepo Yosefe
Ngakhale kuti Yosefe anali kutali na banja lake, Mulungu anaonetsa kuti anali naye.
PHUNZILO 17
Mose Anasankha Kulambila Yehova
Ali mwana, Mose anapulumuka cifukwa amayi ake anacita zinthu mwanzelu.
PHUNZILO 19
Milili Itatu Yoyambilila
Farao anabweletsa mavuto pa anthu ake. Cifukwa conyada, anakana kucita cinthu cosavuta.
PHUNZILO 22
Cozizwitsa pa Nyanja Yofiila
Farao anapulumuka milili 10. Koma kodi anapulumuka cozizwitsa ici ca Mulungu?