Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mawu Ofotokoza Chigawo 5

Mawu Ofotokoza Chigawo 5

Patangotha miyezi iwiri kuchokera pamene anawoloka Nyanja Yofiira, Aisiraeli anafika paphiri la Sinai. Paphirili, Yehova anachita nawo pangano loti akhale anthu ake apadera. Iye ankawateteza komanso kuwapatsa zofunika pa moyo. Ankawapatsa malo abwino oti azikhala, chakudya chothedwa mana komanso zovala zawo sizinkatha. Ngati ndinu kholo, thandizani mwana wanu kudziwa chifukwa chake Yehova anapatsa Aisiraeli Chilamulo, chihema komanso ansembe. Tsindikani ubwino wochita zimene talonjeza, kukhala odzichepetsa komanso okhulupirika kwa Yehova.

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 23

Analonjeza Kuti Azimvera Yehova

Atafika paphiri la Sinai, Aisiraeli analonjeza Mulungu kuti azimumvera.

MUTU 24

Aisiraeli Sanachite Zimene Analonjeza

Mose ali kokatenga Malamulo 10, Aisiraeli anachimwira Mulungu.

MUTU 25

Chihema Cholambiriramo

Mutenti yapadera imeneyi munkakhala likasa la pangano.

MUTU 26

Anthu 12 Anapita Kukaona Dziko la Kanani

Yoswa ndi Kalebe anali osiyana ndi amuna ena 10 omwe anapita kukaona dziko la Kanani.

MUTU 27

Aisiraeli Ena Anaukira Yehova

Kora, Datani, Abiramu, ndi anthu ena 250 analephera kuzindikira mfundo zofunika zokhudza Yehova.

MUTU 28

Bulu wa Balamu Analankhula

Bulu wa Balamu ankaona mngelo amene Balamuyo sankamuona.