Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mawu Oyamba a Cigawo 6

Mawu Oyamba a Cigawo 6

Pamene Aisiraeli anafika ku Dziko Lolonjezedwa, cihema cinakhala likulu lolambililako Yehova m’dzikolo. Ansembe anali kuphunzitsa Cilamulo, ndipo oweluza anali kutsogolela mtundu. Cigawo cino cionetsa mmene zosankha na zocita za munthu zimakhudzila anthu ena. Mwisiraeli aliyense anali na udindo kwa Yehova, komanso kwa munthu mnzake. Onetsani mmene zocita za Debora, Naomi, Yoswa, Hana, mwana wamkazi wa Yefita, na Samueli zinakhudzila anthu ambili. Onetsani kuti ngakhale anthu amene sanali Aisiraeli, monga Rahabi, Rute, Yaeli, komanso Agibeoni, anasankha kukhala kumbali ya Aisiraeli cifukwa anadziŵa kuti Mulungu anali nawo.

M'CIGAWO CINO

PHUNZILO 29

Yehova Asankha Yoswa

Mulungu anapatsa Yoswa malangizo amene na ise angatithandize masiku ano.

PHUNZILO 30

Rahabi Abisa Azondi

Mpanda wa Yeriko unagwa, koma nyumba ya Rahabi siinagwe olo kuti inali yolumikizika ku mpandawo.

PHUNZILO 31

Yoswa na Agibeoni

Yoswa anapemphela kwa Mulungu kuti: “Dzuŵa iwe, ima!” Kodi Mulungu anayankha?

PHUNZILO 32

Mtsogoleli Watsopano na Azimayi Aŵili Olimba Mtima

Pamene Yoswa anamwalila, Aisiraeli anayamba kulambila mafano. Umoyo unali wovuta, koma anathandizidwa kupitila mwa Oweruza Baraki, mneneli wamkazi Debora, na Yaeli amene anaseŵenzetsa cimphompho ca tenthi!

PHUNZILO 33

Rute na Naomi

Akazi aŵili amene amuna awo anafa anabwelela ku isiraeli. Mmodzi wa iwo, Rute, anapita kukakunkha m’minda, kumene Boazi anamuona.

PHUNZILO 34

Gidiyoni Agonjetsa Amidiyani

Amidiyani atapangitsa umoyo wa Aisiraeli kukhala wovuta, Aisiraeli anacondelela Yehova kuti awathandize. Kodi gulu locepa la asilikali a Gidiyoni linacita ciani kuti ligonjetse gulu la adani lokhala na asilikali 135,000?

PHUNZILO 35

Hana Apemphela Kuti Akhale na Mwana

Elikana pamodzi na Hana, Penina na banja lake anapita kukalambila ku cihema ku Silo. Kumeneko Hana anapemphela kuti akhale na mwana. Caka cotsatila iye anabeleka Samueli!

PHUNZILO 36

Lonjezo la Yefita

Kodi Yefita anapanga lonjezo lotani, ndipo cifukwa ciani? Nanga mwana wake anacita ciani atamvela za lonjezo la Atate ake?

PHUNZILO 37

Yehova Akamba na Samueli

Eli Mkulu wa Ansembe, anali ndi ana aamuna aŵili otumikila monga ansembe pa cihema. Iwo sanali kumvela malamulo a Yehova. Koma wacicepele Samueli anali womvela, ndipo Yehova anakamba naye.

PHUNZILO 38

Yehova Anapatsa Mphamvu Samsoni

Mulungu anapatsa mphamvu Samsoni kuti agonjetse Afilisiti, koma pamene Samsoni anapanga cosankha colakwika, Afilisiti anamugwila.