Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mawu Oyamba a Cigawo 7

Mawu Oyamba a Cigawo 7

Cigawo cino cifotokoza mbili ya Mfumu Sauli na Mfumu Davide, pa zaka pafupi-fupi 80. Poyamba, Sauli anali wodzicepetsa komanso woopa Mulungu, koma m’kupita kwa nthawi anasintha na kuleka kukonkha malangizo a Yehova. Ndipo Yehova anamukana. M’kupita kwa nthawi, iye anauza Samueli kudzoza Davide kuti akhale mfumu ya Aisiraeli. Cifukwa ca nsanje, Sauli anayesa kangapo konse kuti aphe Davide, koma Davide sanabwezele. Mwana wa Sauli, Yonatani, anadziŵa kuti Davide anasankhiwa na Yehova. Conco anali wokhulupilika kwa Davide. Olo kuti Davide anacita macimo aakulu, sanakane uphungu wa Yehova. Ngati ndimwe kholo, thandizani mwana wanu kumvetsa kufunika kocilikiza makonzedwe a Mulungu nthawi zonse.

M'CIGAWO CINO

PHUNZILO 39

Mfumu Yoyamba ya Aisiraeli

Mulungu anapatsa Aisiraeli oweluza kuti aziŵatsogolela, koma iwo anafuna mfumu. Samueli anadzoza Sauli kukhala mfumu yoyamba, koma pambuyo pake Yehova anam’kana Sauli. Cifukwa ciani?

PHUNZILO 40

Davide na Goliyati

Yehova asankha Davide kukhala mfumu yotsatila ya Aisiraeli, ndipo Davide aonetsa cifukwa cake anasankhidwa.

PHUNZILO 41

Davide na Sauli

N’cifukwa ciani mmodzi wa anthu awa amazonda mnzake? Nanga mnzakeyo acita zinthu motani?

PHUNZILO 42

Yonatani, Munthu Wolimba Mtima Komanso Wokhulupilika

Mwana wa mfumu akhala bwenzi lapamtima la Davide.

PHUNZILO 43

Chimo ya Mfumu Davide

Kusankha molakwika kumabweletsa mavuto ambili.