Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mawu Ofotokoza Chigawo cha 11

Mawu Ofotokoza Chigawo cha 11

M’chigawochi muli nkhani zochokera m’Malemba Achigiriki. Yesu anabadwira m’banja losauka lomwe linkakhala m’katauni kenakake. Iye ankagwira ntchito yaukalipentala limodzi ndi bambo ake. Koma Yesu anapatsidwa udindo wopulumutsa anthu. Yehova anamusankha kuti akhale Mfumu ya Ufumu wakumwamba. Ngati ndinu kholo, thandizani mwana wanuyo kudziwa kuti Yehova anasankha mwanzeru banja komanso malo oti Yesu abadwire ndiponso akulire. Muthandizeni kudziwa zimene Yehova anachita poteteza Yesu kuti asaphedwe ndi Herode. M’chigawochi tiona umboni wakuti palibe chimene chingalepheretse Yehova kukwaniritsa cholinga chake. Tionanso kuti Yehova anatuma Yohane kuti akonzere Yesu njira. Pokambirana, tsindikani umboni wosonyeza kuti Yesu ankatsatira mfundo za Yehova kuyambira ali mwana ndipo ankazikonda kwambiri.

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 68

Elizabeti Anakhala ndi Mwana

N’chifukwa chiyani mwamuna wa Elizabeti anauzidwa kuti sadzalankhula mpaka mwana atabadwa?

MUTU 69

Gabirieli Anaonekera kwa Mariya

Anamuuza uthenga womwe unasintha moyo wake.

MUTU 70

Angelo Analengeza za Kubadwa kwa Yesu

Angelo atangomva za kubadwa kwa Yesu ananyamuka nthawi yomweyo.

MUTU 71

Yehova Anateteza Yesu

Mfumu yoipa inkafuna kupha Yesu.

MUTU 72

Zimene Yesu Anachita Ali Wamng’ono

Kodi Yesu anachita chiyani kukachisi, zomwe zinadabwitsa aphunzitsi?

MUTU 73

Yohane Anakonza Njira

Yohane atakula anakhala mneneri. Iye ankaphunzitsa kuti Mesiya akubwera. Kodi anthu ankatani akamva uthenga wake?